Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Mafumu 9:1 - Buku Lopatulika

1 Ndipo kunali, atatsiriza Solomoni kumanga nyumba ya Yehova, ndi nyumba ya mfumu, ndi chifuniro chonse cha Solomoni anachikhumbacho,

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Ndipo kunali, atasiriza Solomoni kumanga nyumba ya Yehova, ndi nyumba ya mfumu, ndi chifuniro chonse cha Solomoni anachikhumbacho,

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Tsono Solomoni atamaliza kumanga Nyumba ya Chauta ndi nyumba ya mfumu, ndiponso zonse zimene iye ankafuna kuti amange,

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Solomoni atatsiriza kumanga Nyumba ya Yehova ndi nyumba yaufumu, ndi kukwaniritsa kuchita zonse zimene ankafuna,

Onani mutuwo Koperani




1 Mafumu 9:1
18 Mawu Ofanana  

Ndipo Solomoni anapalana ubwenzi ndi Farao mfumu ya Aejipito, natenga mwana wamkazi wa Farao, nadza naye kumzinda wa Davide, mpaka atamanga nyumba ya iye yekha, ndi nyumba ya Yehova, ndi linga lozinga Yerusalemu.


Maziko ake a nyumba ya Yehova anaikidwa m'chaka chachinai m'mwezi wa Zivi.


Koma nyumba ya iye yekha Solomoni anaimanga zaka khumi mphambu zitatu, natsiriza nyumba yake yonse.


Anamanganso nyumba yotchedwa Nkhalango ya Lebanoni, m'litali mwake munali mikono zana limodzi, kupingasa kwake mikono makumi asanu, ndi msinkhu wake mikono makumi atatu; naisanja pa mizere inai ya mapanda amkungudza, ndi mitanda yamkungudza, ndi mitanda yamkungudza yotanthalika mapandawo.


Motero ntchito zonse zinatsirizika, zimene mfumu Solomoni anachitira nyumba ya Yehova. Ndipo Solomoni analonga zinthu adazipatula Davide atate wake, ndizo siliva ndi golide ndi zipangizo zomwe naziika mosungira chuma cha nyumba ya Yehova.


Tsiku lachisanu ndi chitatu anawauza anthu apite; ndipo iwo anadalitsa mfumu, napita ku mahema ao osekera ndi okondwera mtima chifukwa cha zokoma zonse Yehova anachitira Davide mtumiki wake, ndi Israele anthu ake.


Ndipo kunali, zitatha zaka makumi awiri m'mene Solomoni adatsiriza nyumba ziwirizo, ndizo nyumba ya Yehova ndi nyumba ya mfumu;


popeza Hiramu mfumu ya Tiro adamthandiza Solomoni ndi mitengo yamkungudza ndi yamlombwa ndi golide yemwe, monga momwe iye anafuniramo, chifukwa chake mfumu Solomoni anampatsa Hiramu mizinda makumi awiri m'dziko la Galileya.


ndi mizinda yonse yosungamo zinthu zake za Solomoni, ndi mizinda yosungamo magaleta ake, ndi mizinda yokhalamo apakavalo ake, ndi zina zilizonse zidakomera Solomoni kuzimanga mu Yerusalemu, ndi ku Lebanoni, ndi m'dziko lonse la ufumu wake.


Atatha tsono Solomoni kupemphera, moto unatsika kumwamba, nunyeketsa nsembe yopsereza, ndi nsembe zophera; ndipo ulemerero wa Yehova unadzaza nyumbayi.


Momwemo Solomoni anatsiriza nyumba ya Yehova, ndi nyumba ya mfumu; ndipo zilizonse zidalowa mumtima mwake mwa Solomoni kuzichita m'nyumba ya Yehova, ndi m'nyumba yakeyake, anachita mosalakwitsa.


Ndipo kunali, zitatha zaka makumi awiri m'mene Solomoni anamanga nyumba ya Yehova, ndi nyumba yakeyake,


ndi Baalati, ndi mizinda yonse yosungiramo chuma anali nayo Solomoni, ndi mizinda yonse ya magaleta ake, ndi mizinda ya apakavalo ake, ndi zonse anazifuna Solomoni kuzimanga zomkondweretsa mu Yerusalemu, ndi mu Lebanoni, ndi m'dziko lonse la ufumu wake.


Ndipo chilichonse maso anga anachifuna sindinawamane; sindinakanize mtima wanga chimwemwe chilichonse pakuti mtima wanga unakondwera ndi ntchito zanga zonse; gawo langa la m'ntchito zanga zonse ndi limeneli.


Ndinadzipangira zazikulu; ndinadzimangira nyumba; ndi kuoka mipesa;


Kupenya kwa maso kuposa kukhumba kwa mtima; ichinso ndi chabe ndi kungosautsa mtima.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa