Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Mafumu 8:7 - Buku Lopatulika

7 Popeza akerubiwo anatambasula mapiko ao awiri pamwamba pa likasa, ndipo akerubiwo anaphimba pamwamba pa likasa ndi mphiko zake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Popeza akerubiwo anatambasula mapiko ao awiri pamwamba pa likasa, ndipo akerubiwo anaphimba pamwamba pa likasa ndi mphiko zake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Choncho akerubiwo ankatambasula mapiko ao pamwamba pa Bokosilo, kotero kuti ankaliphimba pamodzi ndi mphiko zake zonyamulira.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Akerubiwo anatambalitsa mapiko awo pamwamba pa Bokosi la Chipangano ndipo anaphimba bokosilo pamodzi ndi mitengo yonyamulira.

Onani mutuwo Koperani




1 Mafumu 8:7
7 Mawu Ofanana  

Ndipo anaika akerubiwo m'chipinda cha m'katimo, ndi mapiko a akerubiwo anatambasuka kotero kuti phiko lake la kerubi mmodzi linajima ku khoma limodzi, ndipo phiko la kerubi wina linajima khoma lina, ndi mapiko ao anagundana pakati pa nyumba.


Ndipo ansembe analonga likasa la chipangano cha Yehova kumalo kwake, ku chipinda chamkati, ku malo opatulika kwambiri, munsi mwa mapiko a akerubi.


Ndipo mphikozo zinatalika kuti nsonga za mphiko zidaoneka ku malo opatulika chakuno cha chipinda chamkati; koma sizinaoneke kubwalo; ndipo zikhala pomwepo mpaka lero lino.


Ndipo akerubi afunyululire mapiko ao m'mwamba, ndi kuphimba chotetezerapo ndi mapiko ao, ndi nkhope zao zipenyane; nkhope za akerubi zipenye kuchotetezerapo.


Pamwamba pa Iye panaima aserafi; yense anali ndi mapiko asanu ndi limodzi; awiri anaphimba nao nkhope yake, awiri naphimba nao mapazi ake, awiri nauluka nao.


ndi kuikapo chophimba cha zikopa za akatumbu; ndi kuyalapo nsalu yamadzi yeniyeni, ndi kupisako mphiko zake.


ndi pamwamba pake akerubi a ulemerero akuchititsa mthunzi pachotetezerapo; za izi sitingathe kunena tsopano paderapadera.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa