Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Mafumu 7:8 - Buku Lopatulika

8 Ndipo nyumba yake yakukhalamo iye, m'bwalo lina la m'tsogolo mwa khondelo, linamangidwa chimodzimodzi. Anammangiranso nyumba mwana wamkazi wa Farao, amene adamkwatira Solomoni, yofanafana ndi khonde limeneli.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Ndipo nyumba yake yakukhalamo iye, m'bwalo lina la m'tsogolo mwa khondelo, linamangidwa chimodzimodzi. Anammangiranso nyumba mwana wamkazi wa Farao, amene adamkwatira Solomoni, yofanafana ndi khonde limeneli.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Tsono nyumba yakeyake kumene ankayenera kukakhalako, adaimanga ku bwalo lina, kumbuyo kwa holo imeneyo. Adaimanga chimodzimodzi ngati holoyo. Ndipo adamanganso chigawo china chofanana ndi holo ya Mpando wachifumu ija kumangira mkazi wake, mwana wa Farao.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Ndipo nyumba yake yodzakhalamo anayimanga kumbuyo kwa chipindacho. Nyumbayo anayimanga mofanana ndi Chipindacho. Solomoni anamanga nyumba inanso yofanana ndi chipindachi, kumangira mkazi wake mwana wa Farao.

Onani mutuwo Koperani




1 Mafumu 7:8
6 Mawu Ofanana  

Ndipo Solomoni anapalana ubwenzi ndi Farao mfumu ya Aejipito, natenga mwana wamkazi wa Farao, nadza naye kumzinda wa Davide, mpaka atamanga nyumba ya iye yekha, ndi nyumba ya Yehova, ndi linga lozinga Yerusalemu.


Izi zonse zinali za miyala ya mtengo wapatali yosemasema, malingana ndi miyeso yake, yocheka ndi mipeni ya manomano m'katimo ndi kunjako, kuyambira kumaziko kufikira kumutu, momwemonso kunjako ku bwalo lalikulu.


Pakuti Farao mfumu ya Aejipito adakwera nalanda Gezere, nautentha ndi moto, nawapha Akanani akukhala m'mzindamo, naupereka kwaulere kwa mwana wake mkazi wa Solomoni.


Koma mwana wamkazi wa Farao anatuluka m'mzinda wa Davide kukwera kunyumba yake adammangira Solomoni, pamenepo iye anamanganso Milo.


Ndipo kunali, asanatulukire Yesaya m'kati mwa mudzi, anamdzera mau a Yehova, ndi kuti,


Ndipo Solomoni anamkweretsa mwana wamkazi wa Farao m'mzinda wa Davide, alowe m'nyumba imene adammangira; pakuti anati, Mkazi wanga asakhale m'nyumba ya Davide mfumu ya Israele; popeza mpopatulika pamene panafika likasa la Yehova.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa