Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Mafumu 7:7 - Buku Lopatulika

7 Ndipo anamanga khonde la mpando wachifumu loweruziramo iye, ndilo khonde la milandu, ndipo linayalidwa ndi mkungudza pansi ndi posanja.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Ndipo anamanga khonde la mpando wachifumu loweruziramo iye, ndilo khonde la milandu, ndipo linayalidwa ndi mkungudza pansi ndi posanja.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Adamanganso chigawo china chachikulu chotchedwa Holo ya Mpando Wachifumu, kapena Holo ya Chiweruzo, modzaweruzira milandu. M'kati mwake adaikuta ndi matabwa amkungudza kuyambira pansi mpaka ku siling'i.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Anamanga chipinda cha mpando waufumu, Chipinda cha Chilungamo, modzaweruziramo milandu ndipo anayikutira ndi matabwa a mkungudza kuchokera pansi mpaka ku denga.

Onani mutuwo Koperani




1 Mafumu 7:7
8 Mawu Ofanana  

Ndipo Aisraele onse anamva maweruzidwe ake idaweruza mfumu, naopa mfumu; pokhala anaona kuti nzeru ya Mulungu inali mwa iye yakuweruza.


Patsani tsono kapolo wanu mtima womvera wakuweruza anthu anu; kuti ndizindikire pakati pa zabwino ndi zoipa; pakuti akutha ndani kuweruza anthu anu ambiri amene?


Ndipo anamanga chipinda cholowera pakhomo pa nyumba ya Kachisiyo, m'litali mwake munali mikono makumi awiri monga m'mimba mwake mwa nyumbayo, kupingasa kwake kunali mikono khumi ku khomo la nyumba.


Pakuti pamenepo anaika mipando ya chiweruzo, mipando ya nyumba ya Davide.


Mfumu yokhala pa mpando woweruzira ipirikitsa zoipa zonse ndi maso ake.


Za kuwonjezera ulamuliro wake, ndi za mtendere sizidzatha pa mpando wachifumu wa Davide, ndi pa ufumu wake, kuukhazikitsa, ndi kuuchirikiza ndi chiweruziro ndi chilungamo kuyambira tsopano ndi kunkabe nthawi zonse. Changu cha Yehova wa makamu chidzachita zimenezi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa