1 Mafumu 7:6 - Buku Lopatulika6 Ndipo anamanga khonde la nsanamira, m'litali mwake munali mikono makumi asanu, kupingasa kwake mikono makumi atatu; ndipo panali khonde lina patsogolo pake, ndi nsanamira ndi mitanda patsogolo pakepo. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20146 Ndipo anamanga khonde la nsanamira, m'litali mwake munali mikono makumi asanu, kupingasa kwake mikono makumi atatu; ndipo panali khonde lina patsogolo pake, ndi nsanamira ndi mitanda patsogolo pakepo. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa6 Panali chigawo chinanso chachikulu chotchedwa Holo ya Nsanamira. M'litali mwake inali ya mamita 22, m'mimba mwake inali ya mamita 13 ndi hafu. Patsogolo pake panali kakhonde ka nsanamira kokhala ndi denga lake. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero6 Iye anapanga Chipinda cha Nsanamira. Mulitali mwake munali mamita 22, mulifupi mwake munali mamita 13 ndi theka. Patsogolo pake panali khonde ndi nsanamira zokhala ndi denga. Onani mutuwo |