Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Mafumu 7:47 - Buku Lopatulika

47 Ndipo Solomoni anazileka zipangizo zonse osaziyesa, popeza zinachuluka ndithu; kulemera kwake kwa mkuwa wonsewo sikunayeseke.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

47 Ndipo Solomoni anazileka zipangizo zonse osaziyesa, popeza zinachuluka ndithu; kulemera kwake kwa mkuwa wonsewo sikunayeseka.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

47 Koma Solomoni adangozisiya ziŵiya zimenezo osaziyesa pa sikelo, chifukwa zidaalipo zambirimbiri. Motero kulemera kwa mkuŵawo sikudadziŵike.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

47 Solomoni sanayeze ziwiya zonsezi chifukwa zinali zambiri ndipo kulemera kwa mkuwa sikunadziwike.

Onani mutuwo Koperani




1 Mafumu 7:47
7 Mawu Ofanana  

Nachotsanso miphika, ndi zoolera, ndi zozimira nyali, ndi zipande, ndi zipangizo zonse zamkuwa zimene anatumikira nazo.


Nsanamira ziwiri, thawale limodzi, ndi maphakawo adazipangira nyumba ya Yehova Solomoni, mkuwa wa zipangizo izi zonse sanakhoze kuyesa kulemera kwake.


Taona tsono, m'kuzunzika kwanga ndinakonzeratu nyumba ya Yehova matalente zikwi zana limodzi a golide, ndi matalente zikwizikwi a siliva, ndi mkuwa, ndi chitsulo, osayesa kulemera kwake, pakuti zidachulukadi; mitengo yomwe ndi miyala ndakonzeratu; nuonjezereko.


golide, ndi siliva, ndi mkuwa, ndi chitsulo, nzosawerengeka; nyamuka, nuchite, Yehova akhale nawe.


Nakonzeratu Davide chitsulo chochuluka cha misomali ya ku zitseko za zipata, ndi ya kuphatikizitsa; ndi mkuwa wochuluka wosauyesa kulemera kwake;


Ndipo Solomoni anazipanga zipangizo izi zonse zochulukadi, pakuti kulemera kwake kwa mkuwa sikunayeseke.


Nsanamira ziwirizo, thawale limodzilo, ndi ng'ombe zamkuwa zinali pansi pa zoikapo, zimene mfumu Solomoni anazipangira nyumba ya Yehova; mkuwa wa zipangizo zonsezi sanathe kuyesa kulemera kwake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa