Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Mafumu 7:20 - Buku Lopatulika

20 Ndipo panalinso mitu pamwamba pa nsanamira ziwirizo, pafupi pa mimbayo, inali m'mbali mwake mwa ukondewo; ndipo makangazawo anali mazana awiri, akukhala mizere yozinga ndanda mutu winawo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

20 Ndipo panalinso mitu pamwamba pa nsanamira ziwirizo, pafupi pa mimbayo, inali m'mbali mwake mwa ukondewo; ndipo makangazawo anali mazana awiri, akukhala mizere yozinga ndanda mutu winawo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

20 Mituyo inali pamwamba pa nsanamira ziŵiri zija, ndiponso pamwamba pa chigawo choulungika cha pambali pake pa ukondewo. Pa mutu umodzi panali makangaza okwanira 200 pa mizere iŵiri yozungulira, ndipo pa mutu winawo panalinso chimodzimodzi.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

20 Pa mitu yonse iwiri ya pamwamba pa nsanamira, pamwamba pa chigawo chonga mʼphika pafupi ndi cholukidwa ngati ukonde, panali makangadza 200 okhala mozungulira mʼmizere.

Onani mutuwo Koperani




1 Mafumu 7:20
7 Mawu Ofanana  

Ndipo mituyi inali pamwamba pa nsanamira za pa chipinda cholowera chinali ngati akakombo malembedwe ake, a mikono inai.


ndi makangaza mazana anai a maukonde awiriwo, mizere iwiri ya makangaza a ukonde umodzi kuphimbira mbale ziwiri za mitu inali pa nsanamirazo,


Msinkhu wake wa nsanamira imodzi ndiwo mikono khumi mphambu isanu ndi itatu, ndi pamwamba pake mutu wamkuwa; ndi msinkhu wake wa mutuwo ndiwo mikono itatu, ndi ukonde, ndi makangaza pamutu pouzinga, zonse zamkuwa; ndi nsanamira inzake inali nazo zomwezo pamodzi ndi ukonde.


Napanga maunyolo a m'chipinda chamkati, nawamanga pa mitu ya nsanamirazi, napanga makangaza zana limodzi, nawamanga pamaunyolo.


ndi makangaza mazana anai a maukonde awiriwa; mizere iwiri ya makangaza ya ukonde uliwonse, akukuta zikho ziwiri za mitu, inali pa nsanamirazo.


Koma nsanamirazo, utali wake wa nsanamira ina unafikira mikono khumi mphambu isanu ndi itatu; ndi chingwe cha mikono khumi ndi iwiri chinaizinga; kuchindikira kwake kunali zala zinai; inali yagweregwere.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa