1 Mafumu 7:2 - Buku Lopatulika2 Anamanganso nyumba yotchedwa Nkhalango ya Lebanoni, m'litali mwake munali mikono zana limodzi, kupingasa kwake mikono makumi asanu, ndi msinkhu wake mikono makumi atatu; naisanja pa mizere inai ya mapanda amkungudza, ndi mitanda yamkungudza, ndi mitanda yamkungudza yotanthalika mapandawo. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20142 Anamanganso nyumba yotchedwa Nkhalango ya Lebanoni, m'litali mwake munali mikono zana limodzi, kupingasa kwake mikono makumi asanu, ndi msinkhu wake mikono makumi atatu; naisanja pa mizere inai ya mapanda amkungudza, ndi mitanda yamkungudza, ndi mitanda yamkungudza yotanthalika mapandawo. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa2 Nyumbayo inali ndi chigawo china chachikulu chotchedwa Nyumba ya Nkhalango ya ku Lebanoni. M'litali mwake inali mamita 44, m'mimba mwake inali mamita 22, msinkhu wake unali mamita 13 ndi theka. Adaimanga pamwamba pa mizere inai ya nsanamira zamkungudza, ndipo panali mitanda yamkungudza pamwamba pa nsanamirazo. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero2 Iye anamanga nyumba yaufumu yotchedwa Nkhalango ya Lebanoni yomwe mulitali mwake inali mamita 44, mulifupi mwake mamita 22, msinkhu wake mamita 13 ndi theka; ndipo inakhazikika pa mizere inayi ya mapanda a mkungudza yokhala ndi mitanda ya mkungudza yotanthalika pa mapandawo. Onani mutuwo |