Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Mafumu 7:12 - Buku Lopatulika

12 Ndipo bwalo lalikulu lozingapo linali ndi mizere itatu ya miyala yosemasema, ndi mzere umodzi wa mitanda yamkungudza, monga bwalo la pakati pa nyumba ya Yehova, ndi chipinda cholowera cha nyumbayo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 Ndipo bwalo lalikulu lozingapo linali ndi mizere itatu ya miyala yosemasema, ndi mzere umodzi wa mitanda yamkungudza, monga bwalo la pakati pa nyumba ya Yehova, ndi chipinda cholowera cha nyumbayo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 Bwalo lalikulu kuzungulira nyumbayo lidamangidwa mizere itatu yamiyala yosemedwa, ndi mzere umodzi wa mitengo yamkungudza. Bwalo lam'kati la nyumbayo ndiponso khonde lake la nyumbayo adazimanga chimodzimodzi.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 Bwalo lalikulu lozungulira nyumbayi linali ndi khoma la mizere itatu ya miyala yosemedwa ndi mzere umodzi wa matabwa a mkungudza. Bwalo la mʼkati la Nyumba ya Yehova ndiponso khonde lake anazimanga mofanana.

Onani mutuwo Koperani




1 Mafumu 7:12
9 Mawu Ofanana  

Ndipo anamanga chipinda cholowera pakhomo pa nyumba ya Kachisiyo, m'litali mwake munali mikono makumi awiri monga m'mimba mwake mwa nyumbayo, kupingasa kwake kunali mikono khumi ku khomo la nyumba.


Ndipo bwalo la m'kati analimanga mizere itatu ya miyala yosemasema, ndi mzere umodzi wa mitanda yamkungudza.


Ndi pamwamba pake panali miyala ya mtengo wapatali, ndiyo miyala yosemasema monga muyeso wake, ndi mitengo yamkungudza.


Ndipo anamanga khonde la nsanamira, m'litali mwake munali mikono makumi asanu, kupingasa kwake mikono makumi atatu; ndipo panali khonde lina patsogolo pake, ndi nsanamira ndi mitanda patsogolo pakepo.


Nalimangira khamu lonse la kuthambo maguwa a nsembe m'mabwalo awiri a nyumba ya Yehova.


Anamanganso bwalo la ansembe, ndi bwalo lalikulu, ndi zitseko za kubwalo, nakuta zitseko zake ndi mkuwa.


Ndipo Yesu analikuyendayenda mu Kachisi m'khonde la Solomoni.


Koma m'mene anagwira Petro ndi Yohane, anawathamangira pamodzi anthu onse kukhonde lotchedwa la Solomoni, alikudabwa ndithu.


Ndipo mwa manja a atumwi zizindikiro ndi zozizwa zambiri zinachitidwa pa anthu; ndipo anali onse ndi mtima umodzi m'khonde la Solomoni.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa