Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Mafumu 6:9 - Buku Lopatulika

9 Momwemo anamanga nyumbayo naitsiriza, naika mitanda, naifolera ndi matabwa amikungudza.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Momwemo anamanga nyumbayo naitsiriza, naika mitanda, naifolera ndi matabwa amikungudza.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Choncho adamanga Nyumbayo mpaka kuimaliza. Ndipo siling'i yake ya Nyumbayo adaipanga ndi mitanda ndi matabwa amkungudza.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Choncho anamanga Nyumbayo mpaka kuyimaliza ndipo denga lake linali la mitanda ndi matabwa a mkungudza.

Onani mutuwo Koperani




1 Mafumu 6:9
8 Mawu Ofanana  

Ndipo anamanga zipindazo zogundana ndi nyumba yonseyo, chipinda chilichonse msinkhu wake mikono isanu; ndipo anazilumikizitsa kunyumba ndi mitengo yamkungudza.


Tsono Solomoni anamanga nyumbayo naitsiriza.


Ndipo m'chaka chakhumi ndi chimodzi m'mwezi wa Buli ndiwo mwezi wachisanu ndi chitatu anatsiriza nyumba konsekonse monga mwa mamangidwe ake onse. Momwemo anaimanga zaka zisanu ndi ziwiri.


Khomo lolowera m'zipinda za pakati linali ku mbali ya ku dzanja lamanja ya nyumba; ndipo anthu amakwerera pa makwerero ozunguniza, kufikira ku zipinda za pakati, ndi kutuluka m'zapakatizo kulowa m'zachitatuzo.


Motero ntchito zonse zinatsirizika, zimene mfumu Solomoni anachitira nyumba ya Yehova. Ndipo Solomoni analonga zinthu adazipatula Davide atate wake, ndizo siliva ndi golide ndi zipangizo zomwe naziika mosungira chuma cha nyumba ya Yehova.


Ndipo chaka chimodzi Solomoni anapereka katatu nsembe zopsereza ndi zamtendere, paguwa la nsembe limene anammangira Yehova, nafukiza zonunkhira paguwa la nsembe pamaso pa Yehova, atatsiriza nyumbayo.


Ndipo anautsa mpanda pozungulira pa chihema ndi guwa la nsembe, napachika nsalu yotsekera pa chipata cha pabwalo. Momwemo Mose anatsiriza ntchitoyi.


Mitanda ya nyumba zathu nja mikungudza, ndi mapaso athu nga mlombwa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa