Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Mafumu 6:3 - Buku Lopatulika

3 Ndipo anamanga chipinda cholowera pakhomo pa nyumba ya Kachisiyo, m'litali mwake munali mikono makumi awiri monga m'mimba mwake mwa nyumbayo, kupingasa kwake kunali mikono khumi ku khomo la nyumba.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Ndipo anamanga chipinda cholowera pakhomo pa nyumba ya Kachisiyo, m'litali mwake munali mikono makumi awiri monga m'mimba mwake mwa nyumbayo, kupingasa kwake kunali mikono khumi ku khomo la nyumba.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Tsono chipinda chakubwalo m'mimba mwake munali mwa mamita asanu ndi anai, kulingana ndi muufupi mwa Nyumbayo. Kutalika kunali kwa mamita anai ndi theka.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Chipinda chakubwalo mʼmbali mwake chinali mamita asanu ndi anayi kulingana ndi mulifupi mwa Nyumbayo ndipo kutalika kwake kunali kwa mamita anayi ndi theka.

Onani mutuwo Koperani




1 Mafumu 6:3
11 Mawu Ofanana  

Ndipo nyumbayo mfumu Solomoni anaimangira Yehova, m'litali mwake munali mikono makumi asanu ndi limodzi, ndi m'mimba mwake mikono makumi awiri, ndi msinkhu wake mikono makumi atatu.


Ndipo m'nyumbamo anamanga mazenera a sefa wokhazikika.


Ndipo bwalo lalikulu lozingapo linali ndi mizere itatu ya miyala yosemasema, ndi mzere umodzi wa mitanda yamkungudza, monga bwalo la pakati pa nyumba ya Yehova, ndi chipinda cholowera cha nyumbayo.


Ndipo anaimiritsa nsanamirazi pa chipinda cholowera cha Kachisi; naimiritsa nsanamira ya ku dzanja lamanja, natcha dzina lake Yakini; naimiritsa nsanamira yakumanzere, natcha dzina lake Bowazi.


Pamenepo Davide anapatsa Solomoni mwana wake chifaniziro cha chipinda cholowera cha Kachisi, ndi cha nyumba zake, ndi cha zosungiramo chuma zake, ndi cha zipinda zosanjikizana zake, ndi cha zipinda zake za m'katimo, ndi cha Kachisi wotetezerepo;


Pamenepo anadza nane kukhonde la Kachisi, nayesa mphuthu za khonde, mikono isanu chakuno, ndi mikono isanu chauko; ndi kupingasa kwa chipata, mikono itatu chakuno, ndi mikono itatu chauko.


Momwemo anayesa m'litali mwake nyumbayo inali kutsogolo kwake kwa mpata wokhala chakuno chake, ndi makonde ake am'mwamba, chakuno ndi chauko, mikono zana limodzi, ndi Kachisi wa m'katimo, ndi makonde a kubwalo;


Pamenepo mdierekezi anamuka naye kumzinda woyera; namuika Iye pamwamba penipeni pa Kachisi,


Ndipo Yesu analikuyendayenda mu Kachisi m'khonde la Solomoni.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa