Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Mafumu 6:2 - Buku Lopatulika

2 Ndipo nyumbayo mfumu Solomoni anaimangira Yehova, m'litali mwake munali mikono makumi asanu ndi limodzi, ndi m'mimba mwake mikono makumi awiri, ndi msinkhu wake mikono makumi atatu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Ndipo nyumbayo mfumu Solomoni anaimangira Yehova, m'litali mwake munali mikono makumi asanu ndi limodzi, ndi m'mimba mwake mikono makumi awiri, ndi msinkhu wake mikono makumi atatu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Nyumba imene mfumu Solomoni adamangira Chauta muutali mwake inali ya mamita 27, muufupi mwake inali ya mamita asanu ndi anai, ndipo msinkhu wake unali wa mamita pafupi 13 ndi theka.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Nyumba imene Solomoni anamangira Yehova mulitali mwake inali mamita 27, mulifupi mwake inali mamita asanu ndi anayi, ndipo msinkhu wake unali mamita 13 ndi theka.

Onani mutuwo Koperani




1 Mafumu 6:2
7 Mawu Ofanana  

Ndipo kunachitika zitapita zaka mazana anai mphambu makumi asanu ndi atatu atatuluka ana a Israele m'dziko la Ejipito, chaka chachinai chakukhala Solomoni mfumu ya Israele, m'mwezi wa Zivi, ndiwo mwezi wachiwiri, iye anayamba kumanga nyumba ya Yehova.


Ndipo anamanga chipinda cholowera pakhomo pa nyumba ya Kachisiyo, m'litali mwake munali mikono makumi awiri monga m'mimba mwake mwa nyumbayo, kupingasa kwake kunali mikono khumi ku khomo la nyumba.


Ndipo maziko adawaika Solomoni akumangapo nyumba ya Mulungu ndi awa: utali wake, kuyesa mikono monga mwa muyeso wakale, ndiwo mikono makumi asanu ndi limodzi, ndi kupingasa kwake mikono makumi awiri.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa