Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Mafumu 5:9 - Buku Lopatulika

9 Akapolo anga adzatsika nayo ku Lebanoni kufika nayo ku nyanja, ndipo ine ndidzaiyandamitsa paphaka kufikira komwe mudzandiuzako, ndi kumeneko ndidzaimasula, ndipo mudzaitenga; nimudzachita chifuniro changa, kumapatsa banja langa zakudya.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Akapolo anga adzatsika nayo ku Lebanoni kufika nayo ku nyanja, ndipo ine ndidzaiyandamitsa paphaka kufikira komwe mudzandiuzako, ndi kumeneko ndidzaimasula, ndipo mudzaitenga; nimudzachita chifuniro changa, kumapatsa banja langa zakudya.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Anthu anga adzatsika nayo kuchokera kuno ku Lebanoni mpaka ku nyanja. Ndipo adzaiyandamitsa pa madzi pa phaka, kuti apite nayo ku malo amene munene. Tsono adzaimasulira kumeneko, ndipo inu mudzailandira. Chofuna ine nchongoti inuyo mudzandipatse chakudya chodyetsa anthu anga.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Anthu anga adzatsika nayo kuchokera ku Lebanoni mpaka ku nyanja, ndipo adzayiyandamitsa pa nyanja mpaka ku malo amene munene. Kumeneko ndidzayimasula ndipo mudzayitenga. Ndipo inu mudzakwaniritsa chokhumba changa pondipatsa chakudya cha banja langa laufumu.”

Onani mutuwo Koperani




1 Mafumu 5:9
14 Mawu Ofanana  

taona, ndachita monga mwa mau ako; taona ndakupatsa mtima wanzeru ndi wakuzindikira, kotero kuti panalibe wina wolingana ndi iwe kale, ndipo sadzakhalanso wina wolingana ndi iwe utamuka.


Ayuda ndi Aisraele anachuluka ngati mchenga wa kunyanja, namadya namamwa namakondwera.


Tsono Hiramu anapatsa Solomoni mitengo yamkungudza ndi mitengo yamlombwa monga momwe anafuniramo.


Ndipo Hiramu anatumiza kwa Solomoni, nati, Ndazimva zija munatumiza kwa inezo, ndidzachita chifuniro chanu chonse, kunena za mitengo yamkungudza ndi mitengo yamlombwa.


Ndipo, Hiramu anatuma anyamata ake m'zombozo amalinyero ozolowera m'nyanja, pamodzi ndi anyamata a Solomoni.


Ndipo mfumu inatero kuti siliva ndi golide zikhale mu Yerusalemu ngati miyala, ndi kuti mikungudza ichuluke ngati mikuyu yokhala kuchidikha.


ndipo ife tidzatema mitengo ku Lebanoni monga mwa kusowa kwanu konse; ndipo tidzabwera nayo kwa inu yoyandamitsa paphaka kufikira ku Yopa; ndipo inu mudzakwera nayo ku Yerusalemu.


Momwemo mfumu Solomoni inaposa mafumu onse a padziko lapansi, kunena za chuma ndi nzeru.


Anaperekanso ndalama kwa amisiri a miyala, ndi a mitengo; ndi chakudya, ndi chakumwa, ndi mafuta, kwa a ku Sidoni, ndi a ku Tiro, kuti atenge mikungudza ku Lebanoni, kufika nayo ku nyanja ku Yopa, monga adawalola Kirusi mfumu ya Persiya.


Koma m'munthu muli mzimu, ndi mpweya wa Wamphamvuyonse wawazindikiritsa.


Ndinalankhula ndi mtima wanga, ndi kuti, Taona, ndakuza ndi kudzienjezera nzeru koposa onse anakhala mu Yerusalemu ndisanabadwe ine; inde mtima wanga wapenyera kwambiri nzeru ndi chidziwitso.


Yuda ndi dziko la Israele anagulana nawe malonda, anagula malonda ako ndi tirigu wa ku Miniti, ndi zozuna, ndi uchi, ndi mafuta, ndi mafuta amankhwala.


Koma Herode anaipidwa nao a ku Tiro ndi Sidoni; ndipo anamdzera iye ndi mtima umodzi, ndipo m'mene adakopa Blasito mdindo wa mfumu, anapempha mtendere, popeza dziko lao linapeza zakudya zochokera ku dziko la mfumu.


Ndioloketu, ndilione dziko lokomali lili tsidya la Yordani, mapiri okoma aja, ndi Lebanoni.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa