1 Mafumu 5:7 - Buku Lopatulika7 Ndipo kunachitika, pamene Hiramu anamva mau ake a Solomoni, anakondwera kwakukulu, nati, Alemekezeke Yehova lero amene wampatsa Davide mwana wanzeru akhale mfumu ya anthu aunyinji amenewa. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20147 Ndipo kunachitika, pamene Hiramu anamva mau ake a Solomoni, anakondwera kwakukulu, nati, Alemekezeke Yehova lero amene wampatsa Davide mwana wanzeru akhale mfumu ya anthu aunyinji amenewa. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa7 Tsono Hiramu atamva mau a Solomoniwo, adakondwa kwambiri, ndipo adati, “Lero Chauta atamandike chifukwa adapatsa Davide mwana wanzeru kuti alamulire mtundu wotchukawu.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero7 Hiramu anakondwa kwambiri atamva uthenga wa Solomoni ndipo anati, “Lero Yehova atamandike chifukwa wapatsa Davide mwana wanzeru kuti alamulire mtundu waukuluwu.” Onani mutuwo |