1 Mafumu 5:6 - Buku Lopatulika6 Ndipo tsono, lamulirani kuti anditemere mitengo yamkungudza ku Lebanoni, ndipo akapolo anga adzakhala ndi akapolo anu, ndipo ndidzakupatsani mphotho ya akapolo anu monga mudzanena; popeza mudziwa kuti pakati pa ife palibe mmisiri wakudziwa kutema mitengo ngati anthu a ku Sidoni. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20146 Ndipo tsono, lamulirani kuti anditemere mitengo yamkungudza ku Lebanoni, ndipo akapolo anga adzakhala ndi akapolo anu, ndipo ndidzakupatsani mphotho ya akapolo anu monga mudzanena; popeza mudziwa kuti pakati pa ife palibe mmisiri wakudziwa kutema mitengo ngati anthu a ku Sidoni. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa6 Nchifukwa chake tsono, mulamule anthu anu kuti andidulire mikungudza ya ku Lebanoni. Tsono anthu anga adzagwira ntchito pamodzi ndi anthu anuwo, ndipo ine ndidzakulipirani chifukwa cha anthu anu malipiro amene mungatchule. Inu mukudziŵa kuti pakati pathupa, palibe munthu wodziŵa kudula mitengo ngati Asidoni.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero6 “Choncho lamulani kuti andidulire mikungudza ya ku Lebanoni. Anthu anga adzagwira ntchito imeneyo pamodzi ndi anthu anuwo, ndipo ine ndidzalipira anthu anuwo malipiro amene inu mungakhazikitse. Inu mukudziwa kuti ife tilibe anthu aluso locheka matabwa monga Asidoni.” Onani mutuwo |
Ndipo m'kati mwa chipindacho, m'litali mwake munali mikono makumi awiri, kupingasa kwake mikono makumi awiri, ndi msinkhu wake mikono makumi awiri, kupingasa kwake mikono makumi awiri, ndi msinkhu wake mikono makumi awiri; ndipo anamukuta ndi golide wayengetsa, nakutanso guwa la nsembe ndi matabwa amkungudza.