Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Mafumu 5:3 - Buku Lopatulika

3 Mudziwa inu kuti atate wanga Davide sanathe kumangira dzina la Yehova Mulungu wake nyumba, chifukwa cha nkhondo zakumzinga konseko, mpaka atawaika Yehova pansi pa mapazi ake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Mudziwa inu kuti atate wanga Davide sanathe kumangira dzina la Yehova Mulungu wake nyumba, chifukwa cha nkhondo zakumzinga konseko, mpaka atawaika Yehova pansi pa mapazi ake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 “Mukudziŵa kuti Davide, bambo wanga, sadathe kumangira nyumba Chauta Mulungu wake, chifukwa cha nkhondo zomwe adani ake adaamzinga nazo mbali zonse. Koma potsiriza Chauta adapereka adani akewo mu ulamuliro wake.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 “Inu mukudziwa kuti chifukwa cha nkhondo zimene zinkachokera ku mbali zonse kulimbana ndi abambo anga, iwo sanathe kumangira Nyumba Yehova Mulungu wawo, mpaka Yehova atawayika adani awo pansi pa ulamuliro wawo.

Onani mutuwo Koperani




1 Mafumu 5:3
17 Mawu Ofanana  

Koma usamange ndiwe nyumbayo, koma mwana wako adzatuluka m'chuuno mwako, iyeyo adzamangira dzina langa nyumba.


Koma mau a Yehova anandidzera, kuti, Wakhetsa mwazi wochuluka, popeza wachita nkhondo zazikulu; sudzamangira dzina langa nyumba, popeza wakhetsa pansi mwazi wambiri pamaso panga;


Ndipo mfumu Davide anaima chilili, nati, Mundimvere ine, abale anga ndi anthu anga, ine kumtima kwanga ndinafuna kulimangira likasa la chipangano la Yehova, ndi popondapo mapazi a Mulungu wathu nyumba yopumulira, ndipo ndidakonzeratu za nyumbayi.


Koma Mulungu anati kwa ine, Sudzamangira dzina langa nyumba, popeza ndiwe munthu wa nkhondo wokhetsa mwazi.


ndi zakudya za pa gome lake, ndi makhalidwe a anyamata ake, ndi maimiriridwe a atumiki ake, ndi mavalidwe ao, ndi makweredwe ake pokwera iye kunka kunyumba ya Yehova, munalibenso moyo mwa iye.


Panalinso podyera ine Ayuda ndi olamulira amuna zana limodzi mphambu makumi asanu, pamodzi ndi iwo akutidzera kuchokera kwa amitundu otizinga.


Zokonzekeratu tsiku limodzi tsono ndizo ng'ombe imodzi, ndi nkhosa zonenepa zisanu ndi imodzi, anandikonzeratunso nkhuku, ndi kamodzi atapita masiku khumi vinyo wambiri wa mitundumitundu; chinkana chonsechi sindinafunsire chakudya cha kazembe, popeza ukapolo unalemerera anthuwo.


Yehova ananena kwa Ambuye wanga, Khalani padzanja lamanja langa, kufikira nditaika adani anu chopondapo mapazi anu.


Munamchititsa ufumu pa ntchito za manja anu; mudagonjetsa zonse pansi pa mapazi ake;


Ndipo mudzapondereza oipa; pakuti adzakhala ngati mapulusa kumapazi anu, tsiku ndidzaikalo, ati Yehova wa makamu.


Pakuti ayenera kuchita ufumu kufikira ataika adani onse pansi pa mapazi ake.


ndipo anakonza zonse pansi pa mapazi ake, nampatsa Iye akhale mutu pamutu pa zonse, kwa Mpingo


ngondo, ndi nswala ndi mphoyo, ndi mphalapala, ndi ngoma, ndi nyumbu, ndi mbalale.


Ndipo kunali, atatulutsira Yoswa mafumu awa, Yoswa anaitana aamuna onse a Israele, ndipo anati kwa akazembe a anthu a nkhondo amene anamuka naye, Yandikirani, pondani pa makosi a mafumu awa. Nayandikira iwo, naponda pa makosi ao.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa