Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Mafumu 4:22 - Buku Lopatulika

22 Ndipo zakudya za Solomoni zofikira tsiku limodzi zinali miyeso makumi atatu ya ufa wosalala, ndi miyeso makumi asanu ndi limodzi ya ufa wamankhupete,

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

22 Ndipo zakudya za Solomoni zofikira tsiku limodzi zinali miyeso makumi atatu ya ufa wosalala, ndi miyeso makumi asanu ndi limodzi ya ufa wamankhupete,

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

22 Chakudya chofunika ku nyumba ya mfumu pa tsiku limodzi chinkakwanira madengu 150 a ufa wosalala ndi madengu 300 a mgaiwa,

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

22 Chakudya cha tsiku ndi tsiku cha Solomoni chinali madengu 150 a ufa wosalala ndi madengu 300 a mgayiwa,

Onani mutuwo Koperani




1 Mafumu 4:22
10 Mawu Ofanana  

ndi zakudya za pa gome lake, ndi makhalidwe a anyamata ake, ndi maimiriridwe a atumiki ake, ndi zovala zao, ndi otenga zikho ake, ndi nsembe yake yopsereza imene amapereka m'nyumba ya Yehova, anakhululuka malungo.


Ndipo Solomoni analamulira maiko onse, kuyambira ku Yufurate kufikira ku dziko la Afilisti ndi ku malire a Ejipito; anthu anabwera nayo mitulo namtumikira Solomoni masiku onse a moyo wake.


ng'ombe zonenepa khumi, ndi ng'ombe za kubusa makumi awiri, ndi nkhosa zana limodzi, osawerenganso ngondo ndi nswala ndi mphoyo ndi mbalame zoweta.


Ndipo Solomoni anapatsa Hiramu miyeso ya tirigu zikwi makumi awiri ndiyo zakudya za banja lake, ndi miyeso makumi awiri ya mafuta oyera; motero Solomoni anapatsa Hiramu chaka ndi chaka.


ndi zakudya za pa gome lake, ndi makhalidwe a anyamata ake, ndi maimiriridwe a atumiki ake, ndi mavalidwe ao, ndi makweredwe ake pokwera iye kunka kunyumba ya Yehova, munalibenso moyo mwa iye.


Zokonzekeratu tsiku limodzi tsono ndizo ng'ombe imodzi, ndi nkhosa zonenepa zisanu ndi imodzi, anandikonzeratunso nkhuku, ndi kamodzi atapita masiku khumi vinyo wambiri wa mitundumitundu; chinkana chonsechi sindinafunsire chakudya cha kazembe, popeza ukapolo unalemerera anthuwo.


Kudziwa kudzaza zipinda zake ndi chuma chonse chofunika cha mtengo wake.


Pochuluka katundu, akudyapo achulukanso; nanga apindulira eni ake chiyani, koma kungopenyera ndi maso ao?


Ndipo mfumu inawaikira gawo la chakudya cha mfumu tsiku ndi tsiku, ndi la vinyo wakumwa iye, ndi kuti awalere zaka zitatu, kuti potsiriza pake aimirire pamaso pa mfumu.


idzawaika akhale otsogolera chikwi, ndi otsogolera makumi asanu; ndipo idzaika ena kulima minda yake, ndi kutema dzinthu zake, ndi kumpangira zipangizo za nkhondo, ndi zipangizo za magaleta.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa