Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Mafumu 4:12 - Buku Lopatulika

12 Baana mwana wa Ahiludi ku Taanaki ndi Megido ndi Beteseani konse, ali pafupi ndi Zaretani kunsi kwa Yezireele, kuyambira ku Beteseani kufikira ku Abele-Mehola, kufikiranso kundunji ku Yokomeamu;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 Baana mwana wa Ahiludi ku Taanaki ndi Megido ndi Beteseani konse, ali pafupi ndi Zaretani kunsi kwa Yezireele, kuyambira ku Beteseani kufikira ku Abele-Mehola, kufikiranso kundunji ku Yokomeamu;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 Baana mwana wa Ahiludi ankayang'anira ku Tanaki, Megido ndi ku Beteseani konse, pafupi ndi Zaretani kunsi kwake kwa Yezireele, ndiponso kuyambira ku Beteseani mpaka ku Abele-Mehola kukafika mpaka ku Yokomeamu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 Baana mwana wa Ahiludi, anali woyangʼanira Taanaki ndi Megido, ndi ku Beti Sani konse, kufupi ndi ku Zaretani kumunsi kwa Yezireeli, kuyambira ku Beti-Seani mpaka ku Abeli-Mehola kukafika mpaka ku Yokineamu;

Onani mutuwo Koperani




1 Mafumu 4:12
13 Mawu Ofanana  

Ndipo dzanja la Yehova linakhala pa Eliya; namanga iye za m'chuuno mwake, nathamanga m'tsogolo mwa Ahabu ku chipata cha Yezireele.


ukadzozenso Yehu mwana wa Nimisi akhale mfumu ya Israele; ukadzozenso Elisa mwana wa Safati wa ku Abele-Mehola akhale mneneri m'malo mwako.


Mfumu inaziyenga pa chidikha cha ku Yordani, m'dothi ladongo, pakati pa Sukoti ndi Zaretani.


ndi Yokomeamu ndi mabusa ake, ndi Betehoroni ndi mabusa ake,


mfumu ya ku Kedesi, imodzi; mfumu ya ku Yokoneamu ku Karimele, imodzi;


Ndipo mu Isakara ndi mu Asere Manase anali nao Beteseani ndi midzi yake, ndi Ibleamu ndi midzi yake, ndi nzika za Dori ndi midzi yake, ndi nzika za Endori ndi midzi yake, ndi nzika za Taanaki ndi midzi yake, ndi nzika za Megido ndi midzi yake; dziko la mapiri atatu.


pamenepo madzi ochokera kumagwero anaima, nauka ngati mulu, kutalitu ku Adama, ndiwo mzinda wa ku mbali ya Zaretani; koma madzi akutsikira kunka ku nyanja ya chidikha, ndiyo Nyanja ya Mchere, anadulidwa konse; ndipo anthu anaoloka pandunji pa Yeriko.


Anadza mafumu nathira nkhondo; pamenepo anathira nkhondo mafumu a Kanani. Mu Taanaki, ku madzi a Megido; osatengako phindu la ndalama.


Ndipo mazana atatuwa anaomba malipenga, ndipo Yehova anakanthanitsa yense mnzake ndi lupanga m'misasa monse; ndi a m'misasa anathawa mpaka ku Betesita ku Zerera, mpaka ku malire a Abele-Mehola pa Tabati.


Koma kunali nthawi imene akadapatsa Merabi mwana wamkazi wa Saulo kwa Davide, iye anapatsidwa kwa Adriyele Mmehola kukhala mkazi wake.


Ndipo anaika zida zake m'nyumba ya Asitaroti; napachika mtembo wake ku linga la ku Beteseani.


ngwazi zonse zinanyamuka ndi kuchezera usiku kuyenda, natenga mtembo wa Saulo, ndi mitembo ya ana ake, pa linga la Beteseani; nafika ku Yabesi-Giliyadi naitentha kumeneko.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa