Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Mafumu 3:8 - Buku Lopatulika

8 Ndipo kapolo wanu ndili pakati pa anthu anu amene Inu munawasankha, anthu ambirimbiri osawerengeka, kapena kulembeka mu unyinji wao.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Ndipo kapolo wanu ndili pakati pa anthu anu amene Inu munawasankha, anthu ambirimbiri osawerengeka, kapena kulembeka m'unyinji wao.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Tsono ine mtumiki wanu ndikukhala pakati pa anthu amene mudaŵasankha, mtundu waukulu, anthu ake ochuluka, oti nkosatheka kuŵaŵerenga.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Mtumiki wanu ali pakati pa anthu amene munawasankha, mtundu waukulu, anthu ochuluka kwambiri osatheka kuwawerenga.

Onani mutuwo Koperani




1 Mafumu 3:8
12 Mawu Ofanana  

Ndipo ndidzayesa mbeu yako monga fumbi lapansi: chotere kuti ngati munthu angathe kuwerenga fumbi lapansi, chomwechonso mbeu yako idzawerengedwa.


Ndipo anamtulutsa iye kunja, nati, Tayang'anatu kumwamba, uwerenge nyenyezi, ngati ukhoza kuziwerenga zimenezo: ndipo anati kwa iye, Zoterezo zidzakhala mbeu zako.


kudalitsa ndidzakudalitsa iwe, kuchulukitsa ndidzachulukitsa mbeu zako monga nyenyezi za kumwamba, monga mchenga wa m'mphepete mwa nyanja; ndipo mbeu zako zidzagonjetsa chipata cha adani ao;


Ayuda ndi Aisraele anachuluka ngati mchenga wa kunyanja, namadya namamwa namakondwera.


Ndipo Davide anati kwa Yowabu ndi kwa akulu a anthu, Kawerengeni Israele kuyambira ku Beereseba kufikira ku Dani; nimundibwezere mau, kuti ndidziwe chiwerengo chao.


Anamtenga kuja anatsata zoyamwitsa, awete Yakobo, anthu ake, ndi Israele, cholowa chake.


Ndipo ndidzatembenukira kwa inu, ndi kukubalitsani, ndi kukuchulukitsani; ndipo ndidzakhazika chipangano changa ndinapangana nanucho.


Pakuti Yehova sadzasiya anthu ake chifukwa cha dzina lake lalikulu; pakuti kudamkomera Yehova kukuyesani inu anthu a Iye yekha.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa