1 Mafumu 3:6 - Buku Lopatulika6 Ndipo Solomoni anati, Munamchitira mtumiki wanu Davide atate wanga zokoma zazikulu, monga umo anayenda pamaso panu ndi choonadi ndi chilungamo ndi mtima woongoka ndi Inu; ndipo mwamsungira chokoma ichi chachikulu kuti mwampatsa mwana kukhala pa mpando wake wachifumu monga lero lino. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20146 Ndipo Solomoni anati, Munamchitira mtumiki wanu Davide atate wanga zokoma zazikulu, monga umo anayenda pamaso panu ndi choonadi ndi chilungamo ndi mtima woongoka ndi Inu; ndipo mwamsungira chokoma ichi chachikulu kuti mwampatsa mwana kukhala pa mpando wake wachifumu monga lero lino. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa6 Solomoni adati, “Inu Mulungu, mudaonetsa chikondi chanu chachikulu ndi chosasinthika kwa mtumiki wanu Davide, bambo wanga, chifukwa choti ankachita zokhulupirika ndi zolungama, ndipo ankayenda moongoka mtima pamaso panu. Ndipo mudamuwonetsabe chikondi chachikulu ndi chosasinthikacho, pakumpatsa mwana amene wakhala pa mpando waufumu wake masiku ano. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero6 Solomoni anayankha kuti, “Inu munaonetsa kukoma mtima kwanu kwakukulu kwa kapolo wanu, abambo anga Davide, chifukwa anali wokhulupirika pamaso panu, wolungama mtima ndiponso wa mtima wangwiro. Inu mukupitirizabe kukoma mtima kwanu kwakukulu kwa iye ndipo mwamupatsa mwana kuti akhale pa mpando wake waufumu lero lino. Onani mutuwo |