Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Mafumu 3:5 - Buku Lopatulika

5 Ku Gibiyoni Yehova anaonekera Solomoni m'kulota usiku, nati Mulungu, Tapempha chimene ndikupatse.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Ku Gibiyoni Yehova anaonekera Solomoni m'kulota usiku, nati Mulungu, Tapempha chimene ndikupatse.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Ku Gibiyoniko Chauta adamuwonekera Solomoni m'maloto usiku, namuuza kuti, “Upemphe chilichonse chimene ufuna kuti ndikupatse.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Ku Gibiyoniko Yehova anaonekera kwa Solomoni mʼmaloto usiku, ndipo Mulungu anati, “Pempha chilichonse chimene ukufuna ndipo ndidzakupatsa.”

Onani mutuwo Koperani




1 Mafumu 3:5
18 Mawu Ofanana  

Ndipo Yehova anakwiya ndi Solomoni, pokhala mtima wake unapatuka kwa Yehova Mulungu wa Israele, amene adamuonekera kawiri,


Yehova anaonekera kwa Solomoni nthawi yachiwiri, monga momwe adamuonekera ku Gibiyoni.


Ndipo anati, Tamvani, tsono mau anga; pakakhala mneneri pakati pa inu, Ine Yehova ndidzizindikiritsa kwa iye m'masomphenya, ndinena naye m'kulota.


Koma pakusinkhasinkha iye zinthu izi, onani, mngelo wa Ambuye anaonekera kwa iye m'kulota, nanena, Yosefe, mwana wa Davide, usaope kudzitengera wekha Maria mkazi wako; pakuti icho cholandiridwa mwa iye chili cha Mzimu Woyera.


Ndipo pamene iwo anachoka, onani, mngelo wa Ambuye anaonekera kwa Yosefe m'kulota, nati, Tauka, nutenge kamwanako ndi amake, nuthawire ku Ejipito, nukakhale kumeneko kufikira ndidzakuuza iwe; pakuti Herode adzafuna kamwana kukaononga Iko.


Koma pakumwalira Herode, onani, mngelo wa Ambuye anaonekera m'kulota kwa Yosefe mu Ejipito,


Ndipo Iye anati kwa iwo, Mufuna kuti ndidzakuchitireni inu chiyani?


Chifukwa chake ndinena ndi inu, Zinthu zilizonse mukazipemphera ndi kuzipempha, khulupirirani kuti mwazilandira, ndipo mudzakhala nazo.


Inu simunandisankhe Ine, koma Ine ndinakusankhani inu, ndipo ndinakuikani, kuti mukamuke inu ndi kubala chipatso, ndi kuti chipatso chanu chikhale; kuti chimene chilichonse mukapempha Atate m'dzina langa akakupatseni inu.


Ngati mukhala mwa Ine, ndi mau anga akhala mwa inu, pemphani chilichonse chimene muchifuna ndipo chidzachitika kwa inu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa