Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Mafumu 3:3 - Buku Lopatulika

3 Ndipo Solomoni anakondana ndi Yehova, nayenda m'malemba a Davide atate wake; koma anaphera nsembe nafukiza zonunkhira pamisanje.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Ndipo Solomoni anakondana ndi Yehova, nayenda m'malemba a Davide atate wake; koma anaphera nsembe nafukiza zonunkhira pamisanje.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Solomoni ankakonda Chauta, namasunga malamulo a Davide bambo wake. Komabe ankapereka nsembe ndi kufukiza lubani ku akachisi aja.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Solomoni anaonetsa chikondi chake pa Yehova poyenda motsatira malamulo a abambo ake Davide, kupatula kuti ankapereka nsembe ndi kufukiza lubani ku malo osiyanasiyana achipembedzo.

Onani mutuwo Koperani




1 Mafumu 3:3
51 Mawu Ofanana  

Koma sindidzalanda ufumu wonse m'dzanja lake, koma ndidzamkhalitsa mfumu masiku ake onse, chifukwa cha Davide mtumiki wanga amene uja ndinamsankha, chifukwa kuti anasunga malamulo anga ndi malemba anga.


Ndipo kudzakhala kuti ukadzamvera iwe zonse ndikulamulirazo, nukadzayenda m'njira zanga ndi kuchita chilungamo pamaso panga, kusunga malemba anga ndi malamulo anga, monga anatero Davide mtumiki wanga pamenepo Ine ndidzakhala ndi iwe, ndidzakumangira ndi kukukhazikitsira nyumba, monga ndinammangira Davide, ndipo ndidzakupatsa iwe Israele.


Ndipo kunali, atakalamba Solomoni, akazi ake anapambutsa mtima wake atsate milungu ina; ndipo mtima wake sunakhale wangwiro ndi Yehova Mulungu wake monga mtima wa Davide atate wake.


Ndipo Solomoni anachita choipa pamaso pa Yehova, osatsata Yehova ndi mtima wonse monga Davide atate wake.


Pakuti anadzimangiranso misanje, ndi zoimiritsa, ndi zifanizo, pa chitunda chonse chachitali, ndi patsinde pa mtengo wogudira uliwonse;


ndipo ndinalanda nyumba ya Davide ufumu, ndi kuupereka kwa iwe, koma sunafanane ndi Davide mtumiki wanga uja, amene anasunga malamulo anga, nanditsata ndi mtima wake wonse kuchita zolunjika zokhazokha pamaso panga;


Ndipo Asa anachita zabwino pamaso pa Yehova monga Davide kholo lake.


Koma misanje sanaichotse, koma mtima wa Asa unali wangwiro ndi Yehova masiku ake onse.


Nayenda iye m'zoipa zonse za atate wake, zimene iye adachita asanalowe ufumu Abiyayo; ndipo mtima wake sunali wangwiro ndi Yehova Mulungu wake monga mtima wa Davide kholo lake.


chifukwa kuti Davide adachita cholungama pamaso pa Yehova, osapatuka masiku ake onse pa zinthu zonse adamlamulira Iye, koma chokhacho chija cha Uriya Muhiti.


Ndipo anayenda m'njira yonse ya atate wake Asa, osapatukamo; nachita choyenera pamaso pa Yehova, koma misanje sanaichotse; anthu anapherabe nsembe, nafukiza zonunkhira pamsanje.


Ndipo Yehosafati anachitana mtendere ndi mfumu ya Israele.


Ndipo ukadzayenda m'njira zanga kusunga malemba anga ndi malamulo anga, monga atate wako Davide anayendamo, Ine ndidzachulukitsa masiku ako.


Ndipo Solomoni anati, Munamchitira mtumiki wanu Davide atate wanga zokoma zazikulu, monga umo anayenda pamaso panu ndi choonadi ndi chilungamo ndi mtima woongoka ndi Inu; ndipo mwamsungira chokoma ichi chachikulu kuti mwampatsa mwana kukhala pa mpando wake wachifumu monga lero lino.


Ndipo tsopano, Yehova Mulungu wa Israele, msungireni mtumiki wanu Davide atate wanga chimene chija mudamlonjezacho, ndi kuti, Sadzakusowa munthu pamaso panga wokhala pa mpando wachifumu wa Israele; komatu ana ako achenjere njira yao, kuti akayende pamaso panga monga umo unayendera iwe pamaso panga.


Mitima yanu ikhale yangwiro ndi Yehova Mulungu wathu, kuyenda m'malemba ake ndi kusunga malamulo ake, monga lero lino.


Ndipo iwe ukadzayenda pamaso panga, monga momwe Davide atate wako anayendera ndi mtima woona ndi wolungama, kuzichita zonse ndakulamulirazo, ndi kusunga malemba anga ndi maweruzo anga,


Koma misanje sanaichotse; anthu anapherabe nsembe, nafukiza kumisanje.


Ndipo Yowasi anati kwa ansembe, Landirani ndalama zonse za zinthu zopatulika azibwera nazo kunyumba ya Yehova, ndizo ndalama za otha msinkhu, ndalama za munthu aliyense monga adamuyesa, ndi ndalama zimene yense azikumbuka m'mtima mwake kuti abwere nazo kunyumba ya Yehova.


Ndipo anachita zoongoka pamaso pa Yehova, koma wosanga Davide kholo lake; nachita monga mwa zonse anazichita Yowasi atate wake.


Koma misanje sanaichotse; anthu anapherabe nsembe, nafukiza pamisanje.


Komatu sanaichotse misanje; anthu anapherabe nsembe, nafukiza pamisanje. Iye anamanga chipata cha kumtunda cha nyumba ya Yehova.


Komatu sanaichotse misanje; anthu anapherabe nsembe, nafukiza pamisanje.


Ndipo mukati kwa ine, Tikhulupirira Yehova Mulungu wathu; sindiye amene Hezekiya wamchotsera misanje yake ndi maguwa a nsembe ake, nati kwa Yuda ndi kwa Yerusalemu, Muzilambira paguwa la nsembe pano mu Yerusalemu?


Anachotsa misanje, naphwanya zoimiritsa, nalikha chifanizo, naphwanya njoka ija yamkuwa adaipanga Mose; pakuti kufikira masiku awa ana a Israele anaifukizira zonunkhira, naitcha Chimkuwa.


Chinkana misanje siinachotsedwe mu Israele, mtima wa Asa unali wangwiro masiku ake onse.


Yehova asunga onse akukondana naye; koma oipa onse adzawaononga.


Kondani Yehova, Inu nonse okondedwa ake, Yehova asunga okhulupirika, ndipo abwezera zochuluka iye wakuchita zodzitama.


kotero kuti ana a Israele azidza nazo nsembe zao, zimene aziphera kuthengo koyera, kuti adze nazo kwa Yehova, ku khomo la chihema chokomanako, kwa wansembe, ndi kuziphera nsembe zoyamika za Yehova.


Ndipo Yesu anati kwa iye, Uzikonda Ambuye Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi nzeru zako zonse.


Ngati mukonda Ine, sungani malamulo anga.


Iye wakukhala nao malamulo anga, ndi kuwasunga, iyeyu ndiye wondikonda Ine; koma wondikonda Ine adzakondedwa ndi Atate wanga, ndipo Ine ndidzamkonda, ndipo ndidzadzionetsa ndekha kwa iye.


Ndipo tidziwa kuti amene akonda Mulungu zinthu zonse zithandizana kuwachitira ubwino, ndiwo amene aitanidwa monga mwa kutsimikiza kwa mtima wake.


Koma ngati wina akonda Mulungu, yemweyu adziwika ndi Iye.


Ndipo tsopano, Israele, Yehova Mulungu wanu afunanji nanu, koma kuti muziopa Yehova Mulungu wanu, kuyenda m'njira zake zonse, ndi kukonda, ndi kutumikira Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse,


kusunga malamulo a Yehova, ndi malemba ake, amene ndikuuzani lero kuti kukukomereni inu?


Ndipo kudzakhala mukasamalira chisamalire malamulo anga amene ndikuuzani lero lino, kukonda Yehova Mulungu wanu, ndi kumtumikira ndi mtima wanu wonse, ndi moyo wanu wonse,


popeza ndikuuzani lero kukonda Yehova Mulungu wanu, kuyenda m'njira zake, ndi kusunga malamulo ake ndi malemba ake ndi maweruzo ake, kuti mukakhale ndi moyo ndi kuchuluka, ndi kuti Yehova Mulungu wanu akakudalitseni m'dziko limene mulowako kulilandira.


kukonda Yehova Mulungu wanu, kumvera mau ake, ndi kummamatira Iye, pakuti Iye ndiye moyo wanu, ndi masiku anu ochuluka; kuti mukhale m'dziko limene Yehova analumbirira makolo anu, Abrahamu, Isaki, ndi Yakobo, kuwapatsa ili.


Ndipo Yehova Mulungu wanu adzakudulani mtima wanu, ndi mtima wa mbeu zanu, kuti mukonde Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse, ndi moyo wanu wonse, kuti mukhale ndi moyo.


ndipo muzikonda Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse, ndi moyo wanu wonse, ndi mphamvu yanu yonse.


Wodala munthu wakupirira poyesedwa; pakuti pamene wavomerezeka, adzalandira korona wa moyo, amene Ambuye adalonjezera iwo akumkonda Iye.


Mverani, abale anga okondedwa; kodi Mulungu sanasankhe osauka a dziko lapansi akhale olemera ndi chikhulupiriro, ndi olowa nyumba a ufumu umene adaulonjeza kwa iwo akumkonda Iye?


Ndipo anawayankha nati, Alipo; onani ali m'tsogolo mwanu; fulumirani pakuti wabwera lero kumzinda kuno; popeza lero anthu akuti aphere nsembe pamsanje;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa