Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Mafumu 3:2 - Buku Lopatulika

2 Koma anthu anaphera nsembe pamisanje, popeza panalibe nyumba yomangira dzina la Yehova kufikira masiku omwewo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Koma anthu anaphera nsembe pamisanje, popeza panalibe nyumba yomangira dzina la Yehova kufikira masiku omwewo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Anthu nsembe ankatsirirabe ku akachisi osiyanasiyana, chifukwa choti nthaŵi imeneyo anali asanammangire nyumba Chauta.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Koma anthu ankaperekabe nsembe ku malo achipembedzo osiyanasiyana chifukwa chakuti mpaka pa nthawi imeneyo Dzina la Yehova anali asanalimangire nyumba.

Onani mutuwo Koperani




1 Mafumu 3:2
17 Mawu Ofanana  

Pakuti anadzimangiranso misanje, ndi zoimiritsa, ndi zifanizo, pa chitunda chonse chachitali, ndi patsinde pa mtengo wogudira uliwonse;


Koma misanje sanaichotse, koma mtima wa Asa unali wangwiro ndi Yehova masiku ake onse.


Ndipo anayenda m'njira yonse ya atate wake Asa, osapatukamo; nachita choyenera pamaso pa Yehova, koma misanje sanaichotse; anthu anapherabe nsembe, nafukiza zonunkhira pamsanje.


Ndipo Yehosafati anachitana mtendere ndi mfumu ya Israele.


Mudziwa inu kuti atate wanga Davide sanathe kumangira dzina la Yehova Mulungu wake nyumba, chifukwa cha nkhondo zakumzinga konseko, mpaka atawaika Yehova pansi pa mapazi ake.


Ndipo Yowasi anati kwa ansembe, Landirani ndalama zonse za zinthu zopatulika azibwera nazo kunyumba ya Yehova, ndizo ndalama za otha msinkhu, ndalama za munthu aliyense monga adamuyesa, ndi ndalama zimene yense azikumbuka m'mtima mwake kuti abwere nazo kunyumba ya Yehova.


Chinkana misanje siinachotsedwe mu Israele, mtima wa Asa unali wangwiro masiku ake onse.


Koma anthu anapherabe nsembe pamisanje; koma anaziphera Yehova Mulungu wao.


Ndipo anautsa mtima wake ndi malo amsanje ao, namchititsa nsanje ndi mafano osema.


Ndipo ndidzaononga malo amsanje anu, ndi kulikha zoimiritsa zanu za dzuwa, ndi kuponya mitembo yanu pa mitembo ya mafano anu; ndi moyo wanga udzanyansidwa nanu.


Dzichenjerani nokha, musamapereka nsembe zanu zopsereza pamalo ponse upaona:


Ndipo anawayankha nati, Alipo; onani ali m'tsogolo mwanu; fulumirani pakuti wabwera lero kumzinda kuno; popeza lero anthu akuti aphere nsembe pamsanje;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa