Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Mafumu 22:41 - Buku Lopatulika

41 Koma Yehosafati mwana wa Asa anayamba kukhala mfumu ya Yuda chaka chachinai cha Ahabu mfumu ya Israele.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

41 Koma Yehosafati mwana wa Asa anayamba kukhala mfumu ya Yuda chaka chachinai cha Ahabu mfumu ya Israele.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

41 Yehosafati, mwana wa Asa, adayamba kulamulira ku Yuda pa chaka chachinai cha ufumu wa Ahabu, mfumu ya ku Israele.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

41 Yehosafati, mwana wa Asa anakhala mfumu ya ku Yuda chaka chachinayi cha Ahabu mfumu ya ku Israeli.

Onani mutuwo Koperani




1 Mafumu 22:41
7 Mawu Ofanana  

Nagona Asa ndi makolo ake, naikidwa kwa makolo ake m'mzinda wa Davide kholo lake; ndipo Yehosafati mwana wake analowa ufumu m'malo mwake.


Koma kunachitika chaka chachitatu, kuti Yehosafati mfumu ya Yuda anatsikira kwa mfumu ya Israele.


Ndipo Ahabu anagona ndi makolo ake; ndi Ahaziya mwana wake anakhala mfumu m'malo mwake.


Yehosafati anali wa zaka makumi atatu mphambu zisanu, pamene analowa ufumu, nakhala mfumu zaka makumi awiri mphambu zisanu mu Yerusalemu. Ndi dzina la amake linali Azuba mwana wa Sili.


Ndipo mwana wa Solomoni ndiye Rehobowamu, Abiya mwana wake, Asa mwana wake, Yehosafati mwana wake,


Ndipo Yehosafati mwana wake anakhala mfumu m'malo mwake, nadzilimbitsa kuyambana ndi Israele.


Momwemo Yehosafati anakhala mfumu ya Yuda; anali wa zaka makumi atatu mphambu zisanu polowa ufumu wake, nakhala mfumu mu Yerusalemu zaka makumi awiri; ndi dzina la make ndiye Azuba mwana wa Sili.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa