Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Mafumu 22:4 - Buku Lopatulika

4 Tsono anati kwa Yehosafati, Kodi udzapita nane kunkhondo ku Ramoti Giliyadi? Ndipo Yehosafati anati kwa mfumu ya Israele, M'mene ukhalira iwe ndi momwe ndikhalira ndine; anthu anga monga anthu ako, akavalo anga monga akavalo ako.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Tsono anati kwa Yehosafati, Kodi udzapita nane kunkhondo ku Ramoti Giliyadi? Ndipo Yehosafati anati kwa mfumu ya Israele, M'mene ukhalira iwe ndi momwe ndikhalira ndine; anthu anga monga anthu ako, akavalo anga monga akavalo ako.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Ndipo adafunsa Yehosafati kuti, “Kodi udzapita nane limodzi ku nkhondo ku Ramoti-Giliyadi?” Yehosafati adauza mfumu ya ku Israeleyo kuti, “Ine ndili nanu limodzi, anthu anga nganu, akavalo anga nganunso.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Tsono iye anafunsa Yehosafati kuti, “Kodi udzapita nane ku nkhondo ku Ramoti Giliyadi?” Yehosafati anayankha mfumu ya ku Israeli kuti, “Ine ndili monga inu, anthu anga monga anthu anu, akavalo anga monga akavalo anu.”

Onani mutuwo Koperani




1 Mafumu 22:4
13 Mawu Ofanana  

Tsono mfumu ya Israele ndi Yehosafati mfumu ya Yuda anakwera ku Ramoti Giliyadi.


Ndipo Yehosafati ananena ndi mfumu ya Israele, Funsira ku mau a Yehova lero.


Benigebere ku Ramoti Giliyadi, iyeyo anali nayo mizinda ya Yairi mwana wa Manase ili mu Giliyadiyo, iye anali nalo dziko la Arigobu lili mu Basani, mizinda yaikulu makumi asanu ndi limodzi yamalinga ndi zitseko zamkuwa;


Nakatumiza mau kwa Yehosafati mfumu ya Yuda, ndi kuti, Mfumu ya Mowabu wapandukana ndi ine; kodi udzamuka nane kukathira nkhondo pa Mowabu? Nati, Ndidzakwera: ine ndikhala ngati iwe, anthu anga ngati anthu ako, akavalo anga ngati akavalo ako.


Nati Ahabu mfumu ya Israele kwa Yehosafati mfumu ya Yuda, Mupita nane kodi ku Ramoti Giliyadi? Nayankha, nati, Monga inu momwemo ine; monga anthu anu momwemo anthu anga; tidzakhala nanu ku nkhondoyi.


Natuluka Yehu mwana wa Hanani mlauli kukomana naye, nati kwa mfumu Yehosafati, Muyenera kodi kuthandiza zoipa, ndi kukonda amene adana ndi Yehova? Chifukwa cha ichi ukugwerani mkwiyo wochokera kwa Yehova.


Ukayenda ndi anzeru udzakhala wanzeru: koma mnzao wa opusa adzaphwetekedwa.


Musanyengedwe; mayanjano oipa aipsa makhalidwe okoma.


ndipo musayanjane nazo ntchito za mdima zosabala kanthu, koma makamakanso muzitsutse;


Pakuti iye wakumpatsa moni ayanjana nazo ntchito zake zoipa.


Ndipo iye amene apambana, ndi iye amene asunga ntchito zanga kufikira chitsiriziro, kwa iye ndidzapatsa ulamuliro wa pa amitundu;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa