Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Mafumu 22:3 - Buku Lopatulika

3 Ndipo mfumu ya Israele ananena ndi anyamata ake, nati, Kodi simudziwa kuti Ramoti Giliyadi ngwathu, ndipo tangokhala chete, osaulanditsa m'dzanja la mfumu ya Aramu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Ndipo mfumu ya Israele ananena ndi anyamata ake, nati, Kodi simudziwa kuti Ramoti Giliyadi ngwathu, ndipo tangokhala chete, osaulanditsa m'dzanja la mfumu ya Aramu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Tsono Ahabu adafunsa aphungu ake kuti, “Ramoti-Giliyadi ndi mzinda wathu, nanga chifukwa chiyani ife tikukhala chete, osaulanda kwa mfumu ya ku Siriya?”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Mfumu ya ku Israeli nʼkuti itawuza atumiki ake kuti, “Kodi inu simukudziwa kuti Ramoti Giliyadi ndi dera lathu ndipo ife palibe chimene tikuchita kuti tilitenge deralo mʼmanja mwa mfumu ya Aramu?”

Onani mutuwo Koperani




1 Mafumu 22:3
10 Mawu Ofanana  

Ndipo Abisalomu amene tinamdzoza mfumu yathu anafa kunkhondo. Chifukwa chake tsono mulekeranji kunena mau akuti abwere nayo mfumuyo?


Tsono mfumu ya Israele ndi Yehosafati mfumu ya Yuda anakwera ku Ramoti Giliyadi.


Benigebere ku Ramoti Giliyadi, iyeyo anali nayo mizinda ya Yairi mwana wa Manase ili mu Giliyadiyo, iye anali nalo dziko la Arigobu lili mu Basani, mizinda yaikulu makumi asanu ndi limodzi yamalinga ndi zitseko zamkuwa;


Ndipo anamuka Yoramu mwana wa Ahabu kukathira nkhondo pa Hazaele mfumu ya Aramu ku Ramoti Giliyadi; ndi Aaramu analasa Yoramu.


Motero Yehu mwana wa Yehosafati mwana wa Nimisi anapandukira Yoramu. Tsono Yoramu atalindira ku Ramoti Giliyadi, iye ndi Aisraele onse, chifukwa cha Hazaele mfumu ya Aramu;


ndiyo Bezeri, m'chipululu, m'dziko lachidikha, ndiwo wa Arubeni; ndi Ramoti mu Giliyadi, ndiwo wa Agadi; ndi Golani, mu Basani, ndiwo wa Amanase.


Ndipo tsidya lija la Yordani kum'mawa kwa Yeriko, anaika Bezeri m'chipululu, kuchidikha, wa fuko la Rubeni, ndi Ramoti mu Giliyadi wa fuko la Gadi, ndi Golani mu Basani wa fuko la Manase.


Ndipo motapira m'fuko la Gadi, Ramoti mu Giliyadi ndi mabusa ake, ndiwo mzinda wopulumukirako wakupha mnzakeyo, ndi Mahanaimu ndi mabusa ake;


Koma wina anauza a ku Gaza, ndi kuti, Samisoni walowa kuno. Pamenepo anamzinga, namlalira usiku wonse pa chipata cha mzinda, nakhala chete usiku wonse ndi kuti, Tidikire mpaka kucha, pamenepo tidzamupha.


Nati iwo, Taukani, tiwakwerere; pakuti tapenya dziko, ndipo taonani, ndilo lokoma ndithu; ndi inu muli chete kodi? Musamachita ulesi kumuka ndi kulowa kulandira dzikolo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa