Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Mafumu 22:10 - Buku Lopatulika

10 Ndipo mfumu ya Israele ndi Yehosafati mfumu ya Yuda anakhala onse awiri, yense pa mpando wachifumu wake, ovala zovala zao zachifumu pabwalo popondera mphesa pa khomo la chipata cha Samariya; ndipo aneneri onse ananenera pamaso pao.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 Ndipo mfumu ya Israele ndi Yehosafati mfumu ya Yuda anakhala onse awiri, yense pa mpando wachifumu wake, ovala zovala zao zachifumu pabwalo popondera mphesa pa khomo la chipata cha Samariya; ndipo aneneri onse ananenera pamaso pao.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 Nthaŵi imeneyo mfumu ya ku Israele ndi Yehosafati mfumu ya ku Yuda adaakhala pa mipando yao yaufumu, atavala zovala zao zaufumu. Pamenepo panali pa bwalo lopererapo tirigu, pa khomo la pa chipata cha Samariya. Ndipo aneneri onse ankalosa pamaso pa mafumuwo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 Atavala mikanjo yawo yaufumu, mfumu ya ku Israeli ndi Yehosafati mfumu ya ku Yuda anakhala pa mipando yawo yaufumu pabwalo lopondera tirigu pafupi ndi chipata cha Samariya, pamodzi ndi aneneri onse akunenera pamaso pawo.

Onani mutuwo Koperani




1 Mafumu 22:10
13 Mawu Ofanana  

Ndipo kunali, litapendeka dzuwa, ananenera kufikira nthawi ya kupereka nsembe; koma panalibe mau, kapena wovomereza, kapena wakuwamvera.


Ndipo mfumu ya Israele inanena ndi Yehosafati, Ine ndidzadzizimbaitsa, ndi kulowa kunkhondo, koma vala iwe zovala zako zachifumu. Ndipo mfumu ya Israele inadzizimbaitsa, nilowa kunkhondo.


Pamenepo mfumu ya Israele inasonkhanitsa aneneri ngati anthu mazana anai, nanena nao, Kodi ndizimuka kukathira nkhondo pa Ramoti Giliyadi, kapena ndileke? Nati iwo, Kweraniko; popeza Ambuye adzaupereka m'dzanja la mfumu.


Tsono mfumu ya Israele anaitana mdindo, nati, Kamtenge msanga Mikaya mwana wa Imila.


Ndipo kunali tsiku lachitatu, Estere anavala zovala zake zachifumu, nakaimirira m'bwalo la m'kati la nyumba ya mfumu, popenyana pa nyumba ya mfumu; ndi mfumu inakhala pa mpando wake wachifumu m'nyumba yachifumu, pandunji polowera m'nyumba.


Koma munatuluka kukaona chiyani? Munthu wovala zofewa kodi? Onani, akuvala zofewa ali m'nyumba zamafumu.


koma mudzikundikire nokha chuma mu Mwamba, pamene njenjete kapena dzimbiri siziononga, ndipo mbala siziboola ndi kuba;


Ndipo tsiku lopangira Herode anavala zovala zachifumu, nakhala pa mpando wachifumu, nawafotokozera iwo mau a pabwalo.


M'mawa mwake tsono, atafika Agripa ndi Berenise ndi chifumu chachikulu, ndipo atalowa momvera milandu, pamodzi ndi akapitao aakulu, ndi amuna omveka a mzindawo, ndipo pakulamulira Fesito, anadza naye Paulo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa