Tsono Asa anatenga siliva yense ndi golide yense anatsala pa chuma cha nyumba ya Yehova, ndi chuma chili m'nyumba ya Yehova chuma chili m'nyumba ya mfumu, nazipereka m'manja mwa anyamata ake; ndipo mfumu Asa anazitumiza kwa Benihadadi mwana wa Tabirimoni, mwana wa Heziyoni mfumu ya Aramu, wakukhala ku Damasiko, nati,