Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Mafumu 2:6 - Buku Lopatulika

6 Chita mwa nzeru yako tsono, osalola mutu wake waimvi utsikire kumanda ndi mtendere.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 Chita mwa nzeru yako tsono, osalola mutu wake waimvi utsikire kumanda ndi mtendere.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 Tsono iwe uchite potsata nzeru zako, koma ndithu usalole kuti afe ndi ukalamba ndi kupita ku manda mwamtendere.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 Iwe uchite kwa iye molingana ndi nzeru zako, koma usalole kuti afe ndi ukalamba ndi kupita ku manda mwamtendere.

Onani mutuwo Koperani




1 Mafumu 2:6
18 Mawu Ofanana  

Ndipo iye anati, Mwana wanga sadzatsikira ndi inu, chifukwa kuti mkulu wake wafa, ndipo watsala iye yekha; ngati choipa chikamgwera iye m'njira m'mene mupitamo, inu mudzatsitsira ndi chisoni imvi zanga kumanda.


Zoonatu mwazi wanu wa miyoyo yanu ndidzafuna; padzanja la zinyama zonse ndidzaufuna: ndi padzanja la munthu, padzanja la mbale wake wa munthu ndidzaufuna moyo wa munthu.


Amene akhetsa mwazi wa munthu, ndi munthunso mwazi wake udzakhetsedwa: chifukwa m'chifanizo cha Mulungu Iye anampanga munthu.


Ndipo ndikali wofooka ine lero, chinkana ndinadzozedwa mfumu; ndipo ana aamuna awa a Zeruya andikakalira mtima; Yehova abwezere wochita choipa monga mwa choipa chake.


Koma uchitire zokoma ana aamuna aja a Barizilai wa ku Giliyadi, akhale pakati pa akudyera pa gome lako, popeza momwemo amenewo anandiyandikira muja ndinalikuthawa Abisalomu mbale wako.


Ndipo tsono, usamuyesera iye wosachimwa, popeza ndiwe munthu wanzeru, ndipo udziwa umo uyenera kumchitira iye, nutsitsire mutu wake waimvi ndi mwazi kumanda.


taona, ndachita monga mwa mau ako; taona ndakupatsa mtima wanzeru ndi wakuzindikira, kotero kuti panalibe wina wolingana ndi iwe kale, ndipo sadzakhalanso wina wolingana ndi iwe utamuka.


Chifukwa chake, taona, ndidzakusonkhanitsa ukhale ndi makolo ako, nudzatengedwa ulowe m'manda mwako mumtendere; ndipo sudzaona m'maso mwako choipa chonse ndidzachifikitsira malo ano. Ndipo anambwezera mfumu mau.


Tapenya wangwiro, ndipo taona woongoka mtima! Pakuti ku matsiriziro ake a munthuyo kuli mtendere.


Mfumu yanzeru ipeta amphulupulu, niyendetsapo njinga ya galeta.


Wopalamula mlandu wakupha munthu adzathawira kudzenje; asamuletse.


Popeza sambwezera choipa chake posachedwa atamtsutsa munthu, ana a anthu atsimikizadi mitima yao kuchita zoipa.


Kulibe mtendere, ati Yehova, kwa oipa.


Iye alowa mumtendere, iwo apuma pa mphasa zao, yense woyenda moongoka.


Palibe mtendere, ati Mulungu wanga, kwa oipa.


Sipadzakhalanso khanda la masiku, pena munthu wokalamba osakwanitsa masiku ake; pakuti mwana adzafa wa zaka zana limodzi; ndipo wochimwa pokhala wa zaka zana limodzi adzatemberedwa.


Ndipo musamaipsa dziko muli m'mwemo; popeza mwazi uipsa dziko; pakuti kulibe kutetezera dziko chifukwa cha mwazi anaukhetsa m'mwemo, koma ndi mwazi wa iye anaukhetsa ndiwo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa