Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Mafumu 2:31 - Buku Lopatulika

31 Ndipo mfumu inati kwa iye, Chita monga umo wanena iye, numkwere, numuike; kuti undichotsere ine ndi nyumba ya atate wanga mwazi uja Yowabu anaukhetsa wopanda chifukwa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

31 Ndipo mfumu inati kwa iye, Chita monga umo wanena iye, numkwere, numuike; kuti undichotsere ine ndi nyumba ya atate wanga mwazi uja Yowabu anaukhetsa wopanda chifukwa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

31 Mfumu idamuyankha kuti, “Kachite monga momwe iye waneneramo. Ukamuphe, ndipo ukamuike m'manda. Motero udzandichotsera ine pamodzi ndi banja la bambo wanga mlandu wa imfa ya anthu amene Yowabu adaŵapha popanda chifukwa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

31 Pamenepo mfumu inalamula Benaya kuti, “Kachite monga iye wanenera. Ukamukanthe ndi kumuyika mʼmanda. Ukatero udzandichotsera ine pamodzi ndi nyumba ya abambo anga mlandu wa anthu osalakwa amene Yowabu anawapha.

Onani mutuwo Koperani




1 Mafumu 2:31
11 Mawu Ofanana  

Ndipo pambuyo pake, pakuchimva Davide, anati, Ine ndi ufumu wanga tikhala osachimwira mwazi wa Abinere mwana wa Nere, nthawi zonse, pamaso pa Yehova;


chilango chigwere pamutu wa Yowabu ndi pa nyumba yonse ya atate wake; ndipo kusasoweke kunyumba ya Yowabu munthu wakukhala nayo nthenda yakukha, kapena wakhate, kapena woyenda ndi ndodo, kapena wakugwa ndi lupanga, kapena wakusowa chakudya.


Nafika Benaya ku chihema cha Yehova, nati kwa iye, Mfumu itero, Tatuluka. Nati, Iai, koma ndifere pompano. Ndipo Benaya anabweza mau kwa mfumu, nati, Yowabu wanena chakuti, nandiyankha mwakutimwakuti.


Ndapenyadi dzulo mwazi wa Naboti ndi mwazi wa ana ake, ati Yehova; ndipo ndikubwezera pamunda pano, ati Yehova. Mtengeni tsono, mumponye pamundapo, monga mwa mau a Yehova.


Koma munthu akachita dala pa mnzake, kumupha monyenga; uzimchotsa ku guwa langa la nsembe, kuti afe.


Wopalamula mlandu wakupha munthu adzathawira kudzenje; asamuletse.


Ndipo musamaipsa dziko muli m'mwemo; popeza mwazi uipsa dziko; pakuti kulibe kutetezera dziko chifukwa cha mwazi anaukhetsa m'mwemo, koma ndi mwazi wa iye anaukhetsa ndiwo.


Koma pamene akunjawo anaona chilombocho chili lende padzanja lake, ananena wina ndi mnzake, Zoona munthuyu ndiye wambanda. Angakhale anapulumuka m'nyanja, chilungamo sichimlola akhale ndi moyo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa