Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Mafumu 2:30 - Buku Lopatulika

30 Nafika Benaya ku chihema cha Yehova, nati kwa iye, Mfumu itero, Tatuluka. Nati, Iai, koma ndifere pompano. Ndipo Benaya anabweza mau kwa mfumu, nati, Yowabu wanena chakuti, nandiyankha mwakutimwakuti.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

30 Nafika Benaya ku chihema cha Yehova, nati kwa iye, Mfumu itero, Tatuluka. Nati, Iai, koma ndifere pompano. Ndipo Benaya anabweza mau kwa mfumu, nati, Yowabu wanena chakuti, nandiyankha mwakutimwakuti.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

30 Choncho Benaya adapita ku hema la Chauta lija, ndipo adauza Yowabuyo kuti, “Mfumu ikukulamula kuti utuluke.” Koma Yowabuyo adati, “Iyai, ine ndifera pompano.” Apo Benaya adakauzanso mfumu zimene Yowabu adaanena.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

30 Choncho Benaya analowa mʼtenti ya Yehova ndipo anati kwa Yowabu, “Mfumu ikuti ‘Tuluka!’ ” Koma iye anayankha kuti, “Ayi, ine ndifera muno.” Benaya anakafotokozera mfumu kuti, “Umu ndi mmene Yowabu wandiyankhira.”

Onani mutuwo Koperani




1 Mafumu 2:30
3 Mawu Ofanana  

Ndipo anamuuza mfumu Solomoni, kuti, Yowabu wathawira ku chihema cha Yehova; ndipo taonani, wakhala ku guwa la nsembe. Pomwepo Solomoni anatuma Benaya mwana wa Yehoyada, nati, Kamkwere.


Ndipo mfumu inati kwa iye, Chita monga umo wanena iye, numkwere, numuike; kuti undichotsere ine ndi nyumba ya atate wanga mwazi uja Yowabu anaukhetsa wopanda chifukwa.


Benaya mwana wa Yehoyada, mwana wa ngwazi ya ku Kabizeeli, wochita zachikulu, anapha ana awiri a Ariyele wa ku Mowabu; anatsikanso, napha mkango m'kati mwa dzenje nyengo ya chipale chofewa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa