Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Mafumu 2:12 - Buku Lopatulika

12 Tsono Solomoni anakhala pa mpando wachifumu wa Davide atate wake, ndipo ufumu wake unakhazikika kwakukulu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 Tsono Solomoni anakhala pa mpando wachifumu wa Davide atate wake, ndipo ufumu wake unakhazikika kwakukulu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 Choncho Solomoni adakhala pa mpando waufumu wa Davide atate ake. Ndipo ufumu wake unali wokhazikika kwambiri.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 Choncho Solomoni anakhala pa mpando waufumu wa abambo ake Davide, ndipo ufumu wake unakhazikika kwambiri.

Onani mutuwo Koperani




1 Mafumu 2:12
13 Mawu Ofanana  

chifukwa chake tsono chikukomereni kudalitsa nyumba ya mnyamata wanu kuti ikhale pamaso panu chikhalire; pakuti Inu, Yehova Mulungu, munachinena; ndipo nyumba ya mnyamata wanu idalitsike ndi dalitso lanu ku nthawi zonse.


Muka nulowe kwa mfumu Davide, nukati kwa iye, Mbuye wanga mfumu, kodi simunalumbirire mdzakazi wanu, ndi kuti, Zedi Solomoni mwana wako adzakhala mfumu nditamuka ine, nadzakhala pa mpando wanga wachifumu? Ndipo Adoniya akhaliranji mfumu?


zedi monga umo ndinalumbirira iwe pa Yehova Mulungu wa Israele, ndi kuti, Zoonadi Solomoni mwana wako adzakhala mfumu nditamuka ine, nadzakhala pa mpando wanga wachifumu m'malo mwa ine, zedi nditero lero lomwe.


Pamenepo mumtsate iye, iye nadzadza nadzakhala pa mpando wanga wachifumu, popeza adzakhala iyeyu mfumu m'malo mwanga; ndipo ndamuika iye akhale mtsogoleri wa Israele ndi Yuda.


Ndiponso Solomoni wakhala pa chimpando cha ufumu.


Pamenepo mfumu inalamulira Benaya mwana wa Yehoyada, ndipo iye anatuluka namkwera, namwalira iye. Ndipo ufumu unakhazikika m'dzanja la Solomoni.


Atakalamba tsono Davide ndi kuchuluka masiku, iye analonga mwana wake Solomoni akhale mfumu ya Israele.


Ndipo Solomoni mwana wa Davide analimbikitsidwa mu ufumu wake, ndipo Yehova Mulungu wake anali naye, namkuza kwakukulu.


Ana ako akasunga chipangano changa ndi mboni yanga imene ndidzawaphunzitsa, ana aonso adzakhala pa mpando wanu kunthawi zonse,


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa