Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Mafumu 18:2 - Buku Lopatulika

2 Ndipo Eliya ananka kukadzionetsa kwa Ahabu. Ndipo njala inali yaikulu mu Samariya.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Ndipo Eliya ananka kukadzionetsa kwa Ahabu. Ndipo njala inali yaikulu m'Samariya.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Motero Eliya adapita kukadziwonetsa kwa Ahabu. Pamenepo nkuti njala itafika pake penipeni ku Samariya.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Choncho Eliya anapita kukadzionetsa kwa Ahabu. Tsono nthawi imeneyi njala inakula kwambiri mu Samariya,

Onani mutuwo Koperani




1 Mafumu 18:2
16 Mawu Ofanana  

Ndipo atapita masiku ambiri, mau a Yehova anafika kwa Eliya chaka chachitatu, nati, Kadzionetse kwa Ahabu, ndipo ndidzatumiza mvula padziko.


Ndipo Ahabu anaitana Obadiya woyang'anira nyumba yake. Koma Obadiya anaopa ndithu Yehova;


Chifukwa chake atero Yehova, Sudzatsika pakama pamene wakwerapo, koma udzafa ndithu. Nachoka Eliya.


Koma mu Samariya munali njala yaikulu; ndipo taonani, anaumangira misasa mpaka mutu wa bulu unagulidwa masekeli a siliva makumi asanu ndi atatu; ndi limodzi la magawo anai la muyeso wa kabu wa zitosi za nkhunda linagulidwa ndi masekeli asiliva asanu.


Yehova ndiye kuunika kwanga ndi chipulumutso changa; ndidzaopa yani? Yehova ndiye mphamvu ya moyo wanga; ndidzachita mantha ndi yani?


Pa Inu, Inu nokha, ndinachimwa, ndipo ndinachichita choipacho pamaso panu; kuti mukhale wolungama pakulankhula Inu, mukhalenso woyera pa kuweruza kwanu.


Tsiku lonse atenderuza mau anga, zolingirira zao zonse zili pa ine kundichitira choipa.


Woipa athawa palibe momthamangitsa; koma olungama alimba mtima ngati mkango.


Ine, Inedi, ndine amene nditonthoza mtima wako; kodi iwe ndani, kuti uopa munthu amene adzafa, ndi mwana wa munthu amene adzakhala ngati udzu;


Ndikatulukira kumunda, taonani ophedwa ndi lupanga! Ndikalowa m'mzinda, taonani odwala ndi njala! Pakuti mneneri ndi wansembe ayendayenda m'dziko osadziwa kanthu.


ndipo mudzachita nayo mphamvu yanu chabe; ndi nthaka yanu siidzapereka zipatso zake, ndi mitengo ya m'dziko siidzabala zobala zake.


Pamene ndithyola mchirikizo wanu wa mkate, akazi khumi adzaphika mkate wanu mu mchembo umodzi, nadzabweza mkate wanu ndi kuuyesa; ndipo mudzadya, koma osakhuta.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa