Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Mafumu 16:8 - Buku Lopatulika

8 Ndipo chaka cha makumi awiri mphambu zisanu ndi chimodzi cha Asa mfumu ya Yuda, Ela mwana wa Baasa analowa ufumu wa Israele ku Tiriza, nakhala mfumu zaka ziwiri.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Ndipo chaka cha makumi awiri mphambu zisanu ndi chimodzi cha Asa mfumu ya Yuda, Ela mwana wa Baasa analowa ufumu wa Israele ku Tiriza, nakhala mfumu zaka ziwiri.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Chaka cha 26 cha ufumu wa Asa wa ku Yuda, Ela mwana wa Baasa adaloŵa ufumu wa ku Israele ku Tiriza, ndipo adalamulira zaka ziŵiri.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Mʼchaka cha 26 cha ufumu wa Asa mfumu ya Yuda, Ela mwana wa Baasa anakhala mfumu ya Israeli, ndipo analamulira ku Tiriza zaka ziwiri.

Onani mutuwo Koperani




1 Mafumu 16:8
12 Mawu Ofanana  

Ndipo panali nkhondo pakati pa Asa ndi Baasa mfumu ya Israele masiku ao onse.


Tsono Baasa mwana wa Ahiya analowa ufumu wa Israele chaka chachitatu cha Asa mfumu ya Yuda, nakhala mfumu ku Tiriza zaka makumi awiri mphambu zinai.


Ndipo chaka cha makumi awiri mphambu zisanu ndi ziwiri cha Asa mfumu ya Yuda, Zimiri anali mfumu masiku asanu ndi awiri ku Tiriza. Ndipo anthu analikumangira misasa Gibetoni wa Afilisti.


Pamenepo anthu a Israele anagawika pakati, anthu ena anatsata Tibini mwana wa Ginati kumlonga ufumu, ena natsata Omuri.


Chaka cha makumi atatu ndi chimodzi cha Asa mfumu ya Yuda, Omuri anayamba kukhala mfumu ya Israele, nakhala zaka khumi ndi ziwiri; ku Tiriza anali mfumu zaka zisanu ndi chimodzi.


Nagona Baasa ndi makolo ake, naikidwa ku Tiriza; ndipo Ela mwana wake analowa ufumu m'malo mwake.


Ndiponso mau a Yehova anadza ndi dzanja la mneneri Yehu mwana wa Hanani, kutsutsa Baasa ndi nyumba yake, chifukwa cha zoipa zonse anazichita iye pamaso pa Yehova; popeza anaputa mkwiyo wake ndi machitidwe a manja ake, nafanana ndi nyumba ya Yerobowamu; ndiponso popeza anaikantha.


Ndipo mnyamata wake Zimiri, ndiye woyang'anira dera lina la magaleta ake, anampangira chiwembu; koma iye anali mu Tiriza kumwa ndi kuledzera m'nyumba ya Ariza, ndiye woyang'anira nyumba mu Tiriza.


Koma anakwera Menahemu mwana wa Gadi kuchokera ku Tiriza, nafika ku Samariya, nakantha Salumu mwana wa Yabesi mu Samariya, namupha; nakhala mfumu m'malo mwake.


Chaka cha makumi asanu a Azariya mfumu ya Yuda, Pekahiya mwana wa Menahemu analowa ufumu wake wa Israele mu Samariya, nakhala mfumu zaka ziwiri.


Amoni anali wa zaka makumi awiri mphambu ziwiri polowa iye ufumu wake, nakhala mfumu zaka ziwiri mu Yerusalemu; ndi dzina la make ndiye Mesulemeti mwana wa Haruzi wa ku Yotiba.


Pochimwa dziko akalonga ake achuluka; koma anthu ozindikira ndi odziwa alikhazikikitsa nthawi yaikulu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa