1 Mafumu 16:2 - Buku Lopatulika2 Popeza ndinakukuza iwe kuchokera kufumbi, ndi kukuika iwe mfumu ya anthu anga Israele, koma iwe unayenda m'njira ya Yerobowamu, ndi kuchimwitsa anthu anga Israele, kuputa mkwiyo wanga ndi machimo ao; Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20142 Popeza ndinakukuza iwe kuchokera kufumbi, ndi kukuika iwe mfumu ya anthu anga Israele, koma iwe unayenda m'njira ya Yerobowamu, ndi kuchimwitsa anthu anga Israele, kuputa mkwiyo wanga ndi machimo ao; Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa2 “Iwe sudaali kanthu konse, ndidachita kukukweza kuti ukhale mtsogoleri wa anthu anga a ku Israele. Komabe tsopano wachimwa ngati Yerobowamu, ndipo waŵachimwitsa anthu a ku Israelewo, mwakuti iwo aputa mkwiyo wanga chifukwa cha kuchimwa kwaoko. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero2 “Ine ndinakukuza kuchokera pa fumbi ndipo ndinakupanga kuti ukhale mtsogoleri wa anthu anga Aisraeli, koma iwe wakhala ukuyenda mʼnjira za Yeroboamu ndi kuchimwitsa anthu anga Aisraeli naputa mkwiyo wanga chifukwa cha machimo awo. Onani mutuwo |
Chifukwa chake mbuye wanga mfumu amvere mau a kapolo wake. Ngati ndi Yehova anakuutsirani inu kutsutsana ndi ine, alandire chopereka; koma ngati ndi ana a anthu, atembereredwe pamaso pa Yehova, pakuti anandipirikitsa lero kuti ndisalandireko cholowa cha Yehova, ndi kuti, Muka, utumikire milungu ina.