Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Mafumu 16:12 - Buku Lopatulika

12 Motero Zimiri anaononga nyumba yonse ya Baasa, monga mwa mau a Yehova, amene ananena akumtsutsa Baasa, mwa dzanja la Yehu mneneri,

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 Motero Zimiri anaononga nyumba yonse ya Baasa, monga mwa mau a Yehova, amene ananena akumtsutsa Baasa, mwa dzanja la Yehu mneneri,

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 Motero Zimuri adaononga banja lonse la Baasa monga momwe Chauta adaalankhulira kudzera mwa Yehu mneneri uja. Paja Yehuyo adaadzudzula Baasa

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 Choncho Zimuri anawononga banja lonse la Baasa, molingana ndi mawu amene Yehova anayankhula motsutsa Baasa kudzera mwa mneneri Yehu,

Onani mutuwo Koperani




1 Mafumu 16:12
11 Mawu Ofanana  

Ndipo anamuika, namlira Aisraele, monga mwa mau a Yehova anawalankhula padzanja la mtumiki wake Ahiya mneneri.


Ndipo panali nkhondo pakati pa Asa ndi Baasa mfumu ya Israele masiku ao onse.


Ndipo mau a Yehova akutsutsa Baasa anadza kwa Yehu mwana wa Hanani, nati,


taona, ndidzachotsa psiti Baasa ndi nyumba yake, ndipo ndidzafanizitsa nyumba yako ndi nyumba ya Yerobowamu mwana wa Nebati.


Ndiponso mau a Yehova anadza ndi dzanja la mneneri Yehu mwana wa Hanani, kutsutsa Baasa ndi nyumba yake, chifukwa cha zoipa zonse anazichita iye pamaso pa Yehova; popeza anaputa mkwiyo wake ndi machitidwe a manja ake, nafanana ndi nyumba ya Yerobowamu; ndiponso popeza anaikantha.


Mbiya ya ufa siidathe, ndi nsupa ya mafuta siinachepe, monga mwa mau a Yehova amene ananenetsa Eliya.


Anabweza malire a Israele kuyambira polowera ku Hamati mpaka ku Nyanja ya Araba, monga mwa mau a Yehova Mulungu wa Israele, amene ananena ndi dzanja la mtumiki wake Yona mwana wa Amitai mneneriyo, ndiye wa Gatihefere.


Momwemo mfumu siinamvere anthuwo; pakuti kusinthaku kudafuma kwa Mulungu, kuti Yehova akhazikitse mau ake, amene ananenetsa Ahiya wa ku Silo kwa Yerobowamu mwana wa Nebati.


Natuluka Yehu mwana wa Hanani mlauli kukomana naye, nati kwa mfumu Yehosafati, Muyenera kodi kuthandiza zoipa, ndi kukonda amene adana ndi Yehova? Chifukwa cha ichi ukugwerani mkwiyo wochokera kwa Yehova.


Machitidwe ena tsono adazichita Yehosafati, zoyamba ndi zotsiriza, taonani, zilembedwa m'buku la mau a Yehu mwana wa Hanani, wotchulidwa m'buku la mafumu a Israele.


Wotumiza mau ndi dzanja la chitsiru adula mapazi ake, namwa zompweteka.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa