Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Mafumu 15:3 - Buku Lopatulika

3 Nayenda iye m'zoipa zonse za atate wake, zimene iye adachita asanalowe ufumu Abiyayo; ndipo mtima wake sunali wangwiro ndi Yehova Mulungu wake monga mtima wa Davide kholo lake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Nayenda iye m'zoipa zonse za atate wake, zimene iye adachita asanalowe ufumu Abiyayo; ndipo mtima wake sunali wangwiro ndi Yehova Mulungu wake monga mtima wa Davide kholo lake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Ndipo Abiyayo adatsatira zoipa zonse zimene ankachita bambo wake. Sadatsate Chauta moona monga Davide kholo lake.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Abiya anachita zoyipa zonse zimene abambo ake anazichita. Sanali wangwiro pamaso pa Yehova Mulungu wake, monga linachitira kholo lake Davide.

Onani mutuwo Koperani




1 Mafumu 15:3
12 Mawu Ofanana  

Nditero popeza iwo anandisiya, napembedza Asitaroti mulungu wa Asidoni, ndi Kemosi mulungu wa Amowabu, ndi Milikomu mulungu wa ana a Amoni, osayenda m'njira zanga, kuchita chimene chiyenera pamaso panga, ndi kusunga malemba anga ndi maweruzo anga, monga umo anatero Davide atate wake.


Ndipo kunali, atakalamba Solomoni, akazi ake anapambutsa mtima wake atsate milungu ina; ndipo mtima wake sunakhale wangwiro ndi Yehova Mulungu wake monga mtima wa Davide atate wake.


Koma misanje sanaichotse, koma mtima wa Asa unali wangwiro ndi Yehova masiku ake onse.


Ndipo ukadzayenda m'njira zanga kusunga malemba anga ndi malamulo anga, monga atate wako Davide anayendamo, Ine ndidzachulukitsa masiku ako.


Ndipo Solomoni anakondana ndi Yehova, nayenda m'malemba a Davide atate wake; koma anaphera nsembe nafukiza zonunkhira pamisanje.


Mukumbukire Yehova kuti ndinayendabe pamaso panu m'choonadi, ndi mtima wangwiro, ndi kuchita zokoma m'kuona kwanu. Nalira Hezekiya kulira kwakukulu.


Ndipo anachita zoongoka pamaso pa Yehova, koma wosachita ndi mtima wangwiro.


Mtima wanga ukhale wangwiro m'malemba anu; kuti ndisachite manyazi.


kuti mtima wake usadzikuze pa abale ake, ndi kuti asapatukire lamulolo, kulamanja kapena kulamanzere; kuti achuluke masiku ake, mu ufumu wake, iye ndi ana ake pakati pa Israele.


Mukhululukire kulakwa kwa mdzakazi wanu; pakuti Yehova adzapatsadi mbuye wanga banja lokhazikika, pakuti mbuyanga amaponya nkhondo za Yehova; ndipo mwa inu simudzapezeka choipa masiku anu onse.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa