Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Mafumu 13:9 - Buku Lopatulika

9 Pakuti potero ndinalamulidwa ndi mau a Yehova, ndi kuti, Usakadye mkate, kapena kumwa madzi, kapena kubwerera njira yomweyo unadzerayo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Pakuti potero ndinalamulidwa ndi mau a Yehova, ndi kuti, Usakadye mkate, kapena kumwa madzi, kapena kubwerera njira yomweyo unadzerayo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Pakuti Chauta adandilamula kuti, ‘Usakadye chakudya chilichonse, kapena kumwa madzi, kapenanso kudzera njira yomwe udaadzera kale pobwera.’ ”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Pakuti Yehova anandilamula kuti, ‘Usakadye chakudya kapena kumwa madzi kapena kubwerera podzera njira imene unayendamo kale.’ ”

Onani mutuwo Koperani




1 Mafumu 13:9
19 Mawu Ofanana  

Ndipo onani, munthu wa Mulungu anachokera ku Yuda mwa mau a Yehova nadza ku Betele; ndipo Yerobowamu anali kuimirira m'mbali mwa guwa la nsembe kufukiza zonunkhira.


Tsono iye anayenda njira ina osabwerera njira yomweyo anaidzera pakudza ku Betele.


Nati iye, Sindingabwerere nawe kukalowa kwanu, kapena kudya mkate, kapena kumwa nawe madzi pano;


Tsono anabwerera naye, nakadya kwao, namwa madzi.


Ndipo munthu wa Mulungu ananena ndi mfumu, Mungakhale mundigawira pakati ndi pakati nyumba yanu, sindilowe kwa inu, kapena kudya mkate, kapena kumwa madzi kuno.


Sindinabwerera kusiya malamulo a pa milomo yake; ndasungitsa mau a pakamwa pake koposa lamulo langalanga.


Mtima wanga usalinge kuchinthu choipa, kuchita ntchito zoipa ndi anthu akuchita zopanda pake; ndipo ndisadye zankhuli zao.


Ndipo ananena ndi khamulo, nati, Chokanitu ku mahema a anthu awa oipa, musamakhudza kanthu kao kalikonse, mungaonongeke m'zochimwa zao zonse.


Ngati mudziwa izi, odala inu ngati muzichita.


Muli abwenzi anga inu, ngati muzichita zimene ndikulamulani inu.


Ndipo ndikudandaulirani, abale, yang'anirani iwo akuchita zopatutsana ndi zophunthwitsa, kosalingana ndi chiphunzitsocho munachiphunzira inu; ndipo potolokani pa iwo.


koma tsopano ndalembera inu kuti musayanjane naye, ngati wina wotchedwa mbale ali wachigololo, kapena wosirira, kapena wopembedza mafano, kapena wolalatira, kapena woledzera, kapena wolanda, kungakhale kukadya naye wotere, iai.


ndipo musayanjane nazo ntchito za mdima zosabala kanthu, koma makamakanso muzitsutse;


Ndipo ndinamva mau ena ochokera Kumwamba, nanena, Tulukani m'menemo, anthu anga; kuti mungayanjane ndi machimo ake, ndi kuti mungalandireko ya miliri yake;


Ndipo Samuele anati, Kodi Yehova akondwera ndi nsembe zopsereza ndi nsembe zophera, monga ndi kumvera mau a Yehova? Taonani, kumvera ndiko kokoma koposa nsembe, kutchera khutu koposa mafuta a nkhosa zamphongo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa