1 Mafumu 13:4 - Buku Lopatulika4 Ndipo kunachitika, pakumva mfumu mau a munthu wa Mulungu amene anawafuula, kutemberera guwa la nsembe mu Betele, Yerobowamu anatansa dzanja lake ali ku guwalo, nati, Mgwireni iye. Ndipo dzanja lake analitansira kwa iye linauma, kuti sanathe kulifunyatitsanso. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20144 Ndipo kunachitika, pakumva mfumu mau a munthu wa Mulungu amene anawafuula, kutemberera guwa la nsembe m'Betele, Yerobowamu anatansa dzanja lake ali ku guwalo, nati, Mgwireni iye. Ndipo dzanja lake analitansira kwa iye linauma, kuti sanathe kulifunyatitsanso. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa4 Mfumu Yerobowamu atamva zimene ankanena mneneri wa Mulungu zija za guwa la ku Betele, adatambalitsa dzanja lake ali kuguwako nati, “Mgwireni.” Pomwepo dzanja lake lomwe adaatambalitsira mneneri wa Mulungu lija lidauma kuti gwa, ndipo sadathenso kulibweza. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero4 Mfumu Yeroboamu atamva zimene munthu wa Mulungu ananena motemberera guwa lansembe ku Beteli, anatambasula dzanja lake ali ku guwako ndipo anati, “Mugwireni!” Koma dzanja limene anatambasula kuloza munthu wa Mulunguyo linawuma kuti gwaa, kotero kuti sanathenso kulibweza. Onani mutuwo |