Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Mafumu 13:3 - Buku Lopatulika

3 Ndipo iye anapatsa chizindikiro tsiku lomwelo, nati, Chizindikiro chimene Yehova ananena ndi ichi, Taonani guwali la nsembe lidzang'ambika, ndi phulusa lili pa ilo lidzatayika.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Ndipo iye anapatsa chizindikiro tsiku lomwelo, nati, Chizindikiro chimene Yehova ananena ndi ichi, Taonani guwali la nsembe lidzang'ambika, ndi phulusa lili pa ilo lidzatayika.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Tsono mneneri uja adapereka chizindikiro pa tsiku lomwelo nati, “Chizindikiro chimene Chauta wanena ndi ichi, ‘Guwali lidzang'ambika ndipo phulusa limene lili pamenepo lidzamwazika.’ ”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Tsiku lomwelo munthu wa Mulungu uja anapereka chizindikiro ichi: “Chizindikiro chimene Yehova wanena ndi ichi: Taonani guwali lidzangʼambika pakati ndipo phulusa lili pamenepo lidzamwazika.”

Onani mutuwo Koperani




1 Mafumu 13:3
16 Mawu Ofanana  

Ndipo kunachitika, pakumva mfumu mau a munthu wa Mulungu amene anawafuula, kutemberera guwa la nsembe mu Betele, Yerobowamu anatansa dzanja lake ali ku guwalo, nati, Mgwireni iye. Ndipo dzanja lake analitansira kwa iye linauma, kuti sanathe kulifunyatitsanso.


Nati Hezekiya kwa Yesaya, Chizindikiro chake nchiyani kuti Yehova adzandichiza, ndi kuti ndidzakwera kunka kunyumba ya Yehova tsiku lachitatu?


Ndipo Mose anayankha nati, Koma taonani, sadzakhulupirira ine, kapena kumvera mau anga; pakuti adzanena, Yehova sanakuonekere iwe.


Ndipo Mose ndi Aroni analowa kwa Farao, nachita monga momwe Yehova adawalamulira; ndipo Aroni anaponya pansi ndodo yake pamaso pa Farao, ndi pamaso pa anyamata ake, ndipo inasanduka chinjoka.


Hezekiya anatinso, Chizindikiro nchiyani, kuti ndidzakwera kunka kunyumba ya Yehova?


Ndipo ichi chidzakhala chizindikiro cha kwa inu, ati Yehova, chakuti Ine ndidzakulangani m'malo muno, kuti mudziwe kuti mau anga adzatsimikizidwatu akuchitireni inu zoipa.


Chifukwa chake Ayuda anayankha nati kwa Iye, Mutionetsera ife chizindikiro chanji, pakuti muchita izi?


Ndipo popeza Ayuda afunsa zizindikiro, ndi Agriki atsata nzeru:


Ndipo anati kwa Iye, Ngati mundikomera mtima mundionetse chizindikiro tsopano chakuti ndi Inu wakunena nane.


Ndipo ichi chimene chidzafikira ana ako awiri Hofeni ndi Finehasi, chidzakhala chizindikiro kwa iwo, tsiku limodzi adzafa iwo onse awiri.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa