Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Mafumu 13:11 - Buku Lopatulika

11 Ndipo ku Betele kunakhala mneneri wokalamba, ndipo mwana wake wina anadzamfotokozera machitidwe onse anawachita munthu wa Mulunguyo tsiku lomwelo mu Betele ndi mau ake anawanena ndi mfumu; inde omwe aja iwo anamfotokozera atate wao.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 Ndipo ku Betele kunakhala mneneri wokalamba, ndipo mwana wake wina anadzamfotokozera machitidwe onse anawachita munthu wa Mulunguyo tsiku lomwelo m'Betele ndi mau ake anawanena ndi mfumu; inde omwe aja iwo anamfotokozera atate wao.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 Tsono ku Betele kunkakhala mneneri wina wokalamba. Ana ake adadza kudzamuuza zonse zimene mneneri wa Mulungu adaachita ku Betele tsiku lija. Adauzanso atate ao mau onse amene mneneri wa Mulungu uja adaauza mfumu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 Tsono ku Beteli kunkakhala mneneri wina wokalamba. Mmodzi mwa ana ake anamufotokozera zonse zomwe munthu wa Mulungu anachita kumeneko tsiku limenelo. Anawuzanso abambo ake zimene ananena kwa mfumu.

Onani mutuwo Koperani




1 Mafumu 13:11
13 Mawu Ofanana  

Tsono iye anayenda njira ina osabwerera njira yomweyo anaidzera pakudza ku Betele.


Ndipo atate wao anati kwa iwo, Wapitira njira yiti? Popeza ana ake adaona njira analowera munthu wa Mulungu anachokera ku Yudayo.


Ndipo onani, anthu anapitapo naona mtembo wogwera m'njiramo, ndi mkango uli chiimire pafupi ndi mtembo, nadzanena m'mzinda m'mene munakhala mneneri wokalamba uja.


Nati iye, Mlekeni, munthu asakhudze mafupa ake. Naleka iwo mafupa ake akhale pamodzi ndi mafupa a mneneri uja anatuluka mu Samariya.


ndiwo aneneri a Israele akunenera za Yerusalemu, nauonera masomphenya a mtendere, pamene palibe mtendere, ati Ambuye Yehova.


Wobadwa ndi munthu iwe, Unenere za aneneri a Israele onenerawo, nuziti nao onenera za m'mtima mwaomwao, Tamverani mau a Yehova.


Ndipo Balamu anakweza maso ake, naona Israele alikukhala monga mwa mafuko ao; ndipo mzimu wa Mulungu unadza pa iye.


Ambiri adzati kwa Ine tsiku lomwelo, Ambuye, Ambuye, kodi sitinanenere mau m'dzina lanu, ndi m'dzina lanunso kutulutsa ziwanda, ndi kuchita m'dzina lanunso zamphamvu zambiri?


Koma ngati munthu sadziwa kuweruza nyumba ya iye yekha, adzasunga bwanji Mpingo wa Mulungu?


koma anadzudzulidwa pa kulakwa kwake mwini; bulu wopanda mau, wolankhula ndi mau a munthu, analetsa kuyaluka kwa mneneriyo.


Ndipo kunali, kuti onse amene anamdziwiratu kale, pakuona ichi chakuti, onani, iye ananenera pamodzi ndi aneneri, anati wina ndi mnzake, Ichi nchiyani chinamgwera mwana wa Kisi? Kodi Saulonso ali mwa aneneri?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa