1 Mafumu 12:2 - Buku Lopatulika2 Ndipo kunali kuti Yerobowamu mwana wa Nebati anachimva akali mu Ejipito, kumene anathawira kuchokera ku maso a Solomoni mfumu, pakuti Yerobowamu anakhala ku Ejipito. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20142 Ndipo kunali kuti Yerobowamu mwana wa Nebati anachimva akali m'Ejipito, kumene anathawira kuchokera ku maso a Solomoni mfumu, pakuti Yerobowamu anakhala ku Ejipito. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa2 Nthaŵi imeneyo nkuti Yerobowamu, mwana wa Nebati, adakali ku Ejipito, momwe adaathaŵira mfumu Solomoni muja. Tsono atamva zaufumuzo, Yerobowamu adabwerera kuchokera ku Ejipitoko. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero2 Yeroboamu mwana wa Nebati anamva zimenezi. Nthawi imeneyo nʼkuti Yeroboamuyo akukhala ku Igupto, pakuti atathawa Mfumu Solomoni iyeyo anakakhala ku Igupto. Onani mutuwo |