Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Mafumu 11:9 - Buku Lopatulika

9 Ndipo Yehova anakwiya ndi Solomoni, pokhala mtima wake unapatuka kwa Yehova Mulungu wa Israele, amene adamuonekera kawiri,

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Ndipo Yehova anakwiya ndi Solomoni, pokhala mtima wake unapatuka kwa Yehova Mulungu wa Israele, amene adamuonekera kawiri,

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Choncho Chauta adakwiyira Solomoni, chifukwa choti mtima wake udaasinthika ndi kusiya Chauta, Mulungu wa Aisraele, amene adamuwonekera kaŵiri konse,

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Choncho Yehova anakwiyira Solomoni chifukwa mtima wake unatembenuka kuchoka kwa Yehova Mulungu wa Israeli, amene anamuonekera kawiri konse.

Onani mutuwo Koperani




1 Mafumu 11:9
20 Mawu Ofanana  

Ndipo pakutuluka malirowo, Davide anatumiza munthu namtenga afike kwao kunyumba yake; ndipo iyeyo anakhala mkazi wake nambalira mwana wamwamuna. Koma Yehova anaipidwa ndi chinthu chimene Davide adachita.


Pomwepo mkwiyo wa Yehova udayaka pa Uza, ndipo Mulungu anamkantha pomwepo, chifukwa cha kusalingiriraku; nafa iye pomwepo pa likasa la Mulungu.


Ndipo momwemo anachitiranso akazi ake onse achilendo, amene amafukizira naphera nsembe milungu yao.


Ku Gibiyoni Yehova anaonekera Solomoni m'kulota usiku, nati Mulungu, Tapempha chimene ndikupatse.


Yehova anaonekera kwa Solomoni nthawi yachiwiri, monga momwe adamuonekera ku Gibiyoni.


Ndipo Mulungu anaipidwa nacho chinthuchi, chifukwa chake Iye anakantha Israele.


Pamenepo mkwiyo wa Yehova unamyakira Mose, ndipo anati, Nanga Aroni Mlevi mbale wako sialipo kodi? Ndidziwa kuti kulankhula alankhula. Ndipo, taona, atuluka kudzakomana ndiwe; ndipo pakuona iwe adzakondwera m'mtima mwake.


Chinjiriza mtima wako koposa zonse uzisunga; pakuti magwero a moyo atulukamo.


Chigololo, ndi vinyo, ndi vinyo watsopano, zichotsa mtima.


Pamenepo Yehova anawapsera mtima iwo; nawachokera Iye.


Koma Yehova anakwiya ndi ine, chifukwa cha inu, sanandimvere ine; ndipo Yehova anati kwa ine, Chikukwanire, usaonjezenso kunena ndi Ine za chinthuchi.


Popeza adzapatutsa mwana wanu aleke kunditsata Ine, kuti atumikire milungu ina; potero Yehova adzapsa mtima pa inu, ndipo adzakuonongani msanga.


Ndipo Yehova anakwiya kwambiri ndi Aroni kumuononga; koma ndinampempherera Aroni nthawi yomweyo.


Mu Horebu momwe munautsa mkwiyo wa Yehova; ndipo Yehova anakwiya nanu kukuonongani.


pakuti Dema wandisiya ine, atakonda dziko lino lapansi, napita ku Tesalonika; Kresike ku Galatiya, Tito ku Dalamatiya.


Kundichititsa chisoni kuti ndinaika Saulo akhale mfumu; pakuti wabwerera wosanditsata Ine, ndipo sanachite malamulo anga. Ndipo Samuele anakwiya; nalira kwa Yehova usiku wonse.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa