Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Mafumu 11:8 - Buku Lopatulika

8 Ndipo momwemo anachitiranso akazi ake onse achilendo, amene amafukizira naphera nsembe milungu yao.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Ndipo momwemo anachitiranso akazi ake onse achilendo, amene amafukizira naphera nsembe mafano ao.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Akazi ake onse achilendo adaŵamangira malo ofukizirapo lubani ndi operekerapo nsembe kwa milungu yao.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Iye anamangiranso malo oterewa akazi ake onse achilendo, amene amafukiza lubani ndi kumapereka nsembe kwa milungu yawo.

Onani mutuwo Koperani




1 Mafumu 11:8
10 Mawu Ofanana  

Ndipo mfumu Solomoni anakonda akazi ambiri achilendo, pamodzi ndi mwana wamkazi wa Farao, akazi a ku Mowabu, ndi a ku Amoni, ndi a ku Edomu, ndi a ku Sidoni, ndi Ahiti;


Pamenepo Solomoni anamangira Kemosi fano lonyansitsa la Amowabu ndi Moleki fano lonyansitsa la ana a Amoni misanje, paphiri lili patsogolo pa Yerusalemu.


Ndipo Yehova anakwiya ndi Solomoni, pokhala mtima wake unapatuka kwa Yehova Mulungu wa Israele, amene adamuonekera kawiri,


Nachotsa m'dziko anyamata aja adama, nachotsanso mafano onse anawapanga atate ake.


Nanga Solomoni mfumu ya Israele sanachimwe nazo zinthu izi? Chinkana mwa amitundu ambiri panalibe mfumu ngati iye, ndi Mulungu wake anamkonda, ndi Mulungu wake anamlonga mfumu ya Aisraele onse; koma ngakhale iye, akazi achilendo anamchimwitsa.


Pakuti mzinda uwu unali woutsa mkwiyo wanga ndi ukali wanga kuyambira tsiku lija anaumanga mpaka lero, kuti ndiuchotse pamaso panga;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa