Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Mafumu 11:4 - Buku Lopatulika

4 Ndipo kunali, atakalamba Solomoni, akazi ake anapambutsa mtima wake atsate milungu ina; ndipo mtima wake sunakhale wangwiro ndi Yehova Mulungu wake monga mtima wa Davide atate wake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Ndipo kunali, atakalamba Solomoni, akazi ake anapambutsa mtima wake atsate milungu ina; ndipo mtima wake sunakhala wangwiro ndi Yehova Mulungu wake monga mtima wa Davide atate wake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Solomoni atakalamba, akazi akewo adamnyengerera kuti azitsata milungu yachilendo. Choncho sadatsate Chauta, Mulungu wake, ndi mtima umodzi, monga ankachitira Davide bambo wake.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Solomoni atakalamba, akazi akewo anakopa mtima wake kuti atsatire milungu ina, ndipo sanatsatire Yehova Mulungu wake ndi mtima wodzipereka, monga unalili mtima wa Davide abambo ake.

Onani mutuwo Koperani




1 Mafumu 11:4
26 Mawu Ofanana  

a mitundu ija Yehova adanena ndi ana a Israele za iwo, kuti, Inu musakalowa kwa iwo, ndipo iwo asadzalowe kwa inu; zedi adzatembenuza mitima yanu kutsata milungu yao; amenewo Solomoni anawaumirira kuwakonda.


Nditero popeza iwo anandisiya, napembedza Asitaroti mulungu wa Asidoni, ndi Kemosi mulungu wa Amowabu, ndi Milikomu mulungu wa ana a Amoni, osayenda m'njira zanga, kuchita chimene chiyenera pamaso panga, ndi kusunga malemba anga ndi maweruzo anga, monga umo anatero Davide atate wake.


Ndipo kudzakhala kuti ukadzamvera iwe zonse ndikulamulirazo, nukadzayenda m'njira zanga ndi kuchita chilungamo pamaso panga, kusunga malemba anga ndi malamulo anga, monga anatero Davide mtumiki wanga pamenepo Ine ndidzakhala ndi iwe, ndidzakumangira ndi kukukhazikitsira nyumba, monga ndinammangira Davide, ndipo ndidzakupatsa iwe Israele.


Ndipo masiku amene Solomoni anakhala mfumu ya Aisraele onse mu Yerusalemu anali zaka makumi anai.


Ndipo Solomoni anachita choipa pamaso pa Yehova, osatsata Yehova ndi mtima wonse monga Davide atate wake.


Ndipo Yehova anakwiya ndi Solomoni, pokhala mtima wake unapatuka kwa Yehova Mulungu wa Israele, amene adamuonekera kawiri,


Ndipo Rehobowamu mwana wa Solomoni anali mfumu ya dziko la Yuda. Rehobowamu anali wa zaka makumi anai mphambu chimodzi polowa ufumu wake, nakhala mfumu zaka khumi mphambu zisanu ndi ziwiri mu Yerusalemu, m'mzinda m'mene Yehova adausankha m'mafuko onse a Israele kukhazikamo dzina lake. Ndipo dzina la amake linali Naama Mwamoni.


Koma misanje sanaichotse, koma mtima wa Asa unali wangwiro ndi Yehova masiku ake onse.


Nayenda iye m'zoipa zonse za atate wake, zimene iye adachita asanalowe ufumu Abiyayo; ndipo mtima wake sunali wangwiro ndi Yehova Mulungu wake monga mtima wa Davide kholo lake.


Ndipo Solomoni anakondana ndi Yehova, nayenda m'malemba a Davide atate wake; koma anaphera nsembe nafukiza zonunkhira pamisanje.


Ndipo kunachitika zitapita zaka mazana anai mphambu makumi asanu ndi atatu atatuluka ana a Israele m'dziko la Ejipito, chaka chachinai chakukhala Solomoni mfumu ya Israele, m'mwezi wa Zivi, ndiwo mwezi wachiwiri, iye anayamba kumanga nyumba ya Yehova.


Mitima yanu ikhale yangwiro ndi Yehova Mulungu wathu, kuyenda m'malemba ake ndi kusunga malamulo ake, monga lero lino.


Ndipo kunali, zitatha zaka makumi awiri m'mene Solomoni adatsiriza nyumba ziwirizo, ndizo nyumba ya Yehova ndi nyumba ya mfumu;


Ndipo iwe ukadzayenda pamaso panga, monga momwe Davide atate wako anayendera ndi mtima woona ndi wolungama, kuzichita zonse ndakulamulirazo, ndi kusunga malemba anga ndi maweruzo anga,


Mukumbukire Yehova kuti ndinayendabe pamaso panu m'choonadi, ndi mtima wangwiro, ndi kuchita zokoma m'kuona kwanu. Nalira Hezekiya kulira kwakukulu.


Ndipo iwe Solomoni mwana wanga, umdziwe Mulungu wa atate wako, umtumikire ndi mtima wangwiro ndi moyo waufulu; pakuti Yehova asanthula mitima yonse, nazindikira zolingirira zonse za maganizo; ukamfunafuna Iye udzampeza, koma ukamsiya Iye adzakusiya kosatha.


nimupatse Solomoni mwana wanga mtima wangwiro kusunga malamulo anu, mboni zanu, ndi malemba anu, ndi kuchita izi zonse, ndi kumanga chinyumbachi chimene ndakonzeratu mirimo yake.


Ndipo Yehova anali ndi Yehosafati, popeza anayenda m'njira zake zoyamba za kholo lake Davide, osafuna Abaala;


Ndipo anachita zoongoka pamaso pa Yehova, koma wosachita ndi mtima wangwiro.


Nachita zoongoka pamaso pa Yehova, nayenda m'njira za Davide kholo lake, osapatuka kudzanja lamanja kapena kulamanzere.


Usakhale nayo milungu ina koma Ine ndekha.


Ndipo asadzichulukitsire akazi, kuti ungapatuke mtima wake; kapena asadzichulukitsire kwambiri siliva ndi golide.


Popeza adzapatutsa mwana wanu aleke kunditsata Ine, kuti atumikire milungu ina; potero Yehova adzapsa mtima pa inu, ndipo adzakuonongani msanga.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa