1 Mafumu 11:2 - Buku Lopatulika2 a mitundu ija Yehova adanena ndi ana a Israele za iwo, kuti, Inu musakalowa kwa iwo, ndipo iwo asadzalowe kwa inu; zedi adzatembenuza mitima yanu kutsata milungu yao; amenewo Solomoni anawaumirira kuwakonda. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20142 a mitundu ija Yehova adanena ndi ana a Israele za iwo, kuti, Inu musakalowa kwa iwo, ndipo iwo asadzalowe kwa inu; zedi adzatembenuza mitima yanu kutsata milungu yao; amenewo Solomoni anawaumirira kuwakonda. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa2 Akazi ameneŵa anali a mitundu ija imene Chauta adaauza Aisraele kuti, “Musadzakwatire akazi a mitundu imeneyi, ndipo amuna amitunduyo asadzakwatire akazi a mtundu wanu, poti ndithudi iwowo adzatembenuza mitima yanu, kuti muzitsata milungu yao.” Koma Solomoni ankakondabe akazi a mitundu imeneyo. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero2 Akazi amenewa anali ochokera ku mitundu ija imene Yehova anawuza Aisraeli kuti, “Simuyenera kudzakwatirana nawo amenewa, chifukwa ndithu, amenewa adzatembenuza mitima yanu kuti mutsatire milungu yawo.” Komabe Solomoni anawakonda kwambiri akazi amenewa. Onani mutuwo |