Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Mafumu 10:8 - Buku Lopatulika

8 Odala anthu anu, odala anyamata anu akukhala nthawi zonse pamaso panu, akumvaimva nzeru yanu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Odala anthu anu, odala anyamata anu akukhala nthawi zonse pamaso panu, akumvaimva nzeru yanu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Ngodala anthu anu. Ngodala atumiki anuŵa, amene amaima pamaso panu nthaŵi zonse ndi kumamva nzeru zanu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Ngodala anthu anu! Ngodala atumiki anu amene amayimirira pamaso panu nthawi zonse ndi kumamva nzeru zanu!

Onani mutuwo Koperani




1 Mafumu 10:8
12 Mawu Ofanana  

Koma sindinakhulupirire mau amenewo mpaka ndafika ine kuno, ndaona ndi maso anga; ndipo taonani, anangondiuza dera lina lokha; nzeru zanu ndi zokoma zanu zakula pa mbiri ndinaimvayo.


Ndipo mfumu Rehobowamu anafunsira kwa mandoda, amene anaimirira pamaso pa Solomoni atate wake, akali moyo iyeyo, nati, Inu mundipangire bwanji kuti ndiyankhe anthu awa?


Milomo ya wolungama imadyetsa ambiri; koma zitsiru zimafa posowa nzeru.


Ukayenda ndi anzeru udzakhala wanzeru: koma mnzao wa opusa adzaphwetekedwa.


Kodi upenya munthu wofulumiza ntchito zake? Adzaima pamaso pa mafumu, osaima pamaso pa anthu achabe.


Ngwodala amene andimvera, nadikira pa zitseko zanga tsiku ndi tsiku, ndi kulinda pa mphuthu za makoma anga;


Koma ine, taonani, ndidzakhala pa Mizipa, ndiima pamaso pa Ababiloni, amene adzadza kwa ife; koma inu sonkhanitsani vinyo ndi zipatso zamalimwe ndi mafuta, muziike m'mbiya zanu, nimukhale m'mizinda imene mwailanda.


Koma Iye anati, Inde, koma odala iwo akumva mau a Mulungu, nawasunga.


Mfumu yaikazi ya kumwera idzaimirira pa mlandu wotsiriza pamodzi ndi amuna a mbadwo uno, nadzawatsutsa; pakuti anadza kuchokera kumalekezero a dziko kudzamva nzeru za Solomoni; ndipo onani, woposa Solomoni ali pano.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa