Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Mafumu 10:7 - Buku Lopatulika

7 Koma sindinakhulupirire mau amenewo mpaka ndafika ine kuno, ndaona ndi maso anga; ndipo taonani, anangondiuza dera lina lokha; nzeru zanu ndi zokoma zanu zakula pa mbiri ndinaimvayo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Koma sindinakhulupirira mau amenewo mpaka ndafika ine kuno, ndaona ndi maso anga; ndipo taonani, anangondiuza dera lina lokha; nzeru zanu ndi zokoma zanu zakula pa mbiri ndinaimvayo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Zimenezo sindidazikhulupirire, mpaka nditafika ndi kuziwona chamaso. Ndipotu anthu sadaandiwuze zonse, ngakhale ndi theka lomwe. Nzeru zanu ndiponso zabwino zimene muli nazo zikuposa zimene ndinkazimva.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Koma sindinakhulupirire zinthu zimenezo mpaka nditafika ndi kuona ndi maso anga. Kunena zoona sanandiwuze ngakhale theka lomwe, pakuti nzeru ndi chuma zimene muli nazo zaposa zimene ndinamva.

Onani mutuwo Koperani




1 Mafumu 10:7
9 Mawu Ofanana  

Ndipo anati kwa mfumu, Idali yoonadi mbiri ija ndinaimva ine ku dziko langa ya machitidwe anu ndi nzeru zanu.


Odala anthu anu, odala anyamata anu akukhala nthawi zonse pamaso panu, akumvaimva nzeru yanu.


Tidalingalira zachifundo chanu, Mulungu, m'kati mwa Kachisi wanu.


Pakuti kuyambira kale anthu sanamve pena kumvetsa ndi khutu, ngakhale diso silinaone Mulungu wina popanda Inu, amene amgwirira ntchito iye amene amlindirira Iye.


Pakuti ukoma wake ndi waukulu ndithu, ndi kukongola kwake nkwakukulu ndithu! Tirigu adzakometsera anyamata, ndi vinyo watsopano anamwali.


Ndipo iwowo, pamene anamva kuti ali moyo, ndi kuti adapenyeka kwa iye, sanamvere.


koma monga kulembedwa, Zimene diso silinazione, ndi khutu silinazimve, nisizinalowe mu mtima wa munthu, zimene zilizonse Mulungu anakonzereratu iwo akumkonda Iye.


Okondedwa, tsopano tili ana a Mulungu, ndipo sichinaoneke chimene tidzakhala. Tidziwa kuti, pa kuoneka Iye, tidzakhala ofanana ndi Iye, Pakuti tidzamuona Iye monga ali.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa