1 Mafumu 10:5 - Buku Lopatulika5 ndi zakudya za pa gome lake, ndi makhalidwe a anyamata ake, ndi maimiriridwe a atumiki ake, ndi zovala zao, ndi otenga zikho ake, ndi nsembe yake yopsereza imene amapereka m'nyumba ya Yehova, anakhululuka malungo. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20145 ndi zakudya za pa gome lake, ndi makhalidwe a anyamata ake, ndi maimiriridwe a atumiki ake, ndi zovala zao, ndi otenga zikho ake, ndi nsembe yake yopsereza imene amapereka m'nyumba ya Yehova, anakhululuka malungo. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa5 chakudya cha patebulo pake, m'mene zinkakhalira nduna zake, m'mene ankasungira mwambo atumiki ake ndi zovala zao, atumiki ake operekera zakumwa, ndiponso nsembe zake zopsereza zimene ankapereka ku Nyumba ya Chauta, mfumukaziyo idangoti kukamwa pululu, kusoŵa chonena. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero5 chakudya cha pa tebulo pake, moyo wa antchito ake ndi zovala zawo, atumiki opereka zakumwa, ndiponso nsembe zopsereza zimene ankapereka ku Nyumba ya Yehova, inathedwa nzeru. Onani mutuwo |
napenya, ndi kuona mfumu inaima pa nsanamira yake polowera; ndi atsogoleri, ndi malipenga, anali kwa mfumu; ndi anthu onse a m'dziko anakondwera, naomba amalipenga; oimbira omwe analiko ndi zoimbirazo, nalangiza poimbira cholemekeza. Pamenepo Ataliya anang'amba zovala zake, nati, Chiwembu, chiwembu.