Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Mafumu 10:2 - Buku Lopatulika

2 Nafika ku Yerusalemu ndi ulendo wake waukulu, ndi ngamira zakunyamula zonunkhira, ndi golide wambiri, ndi timiyala ta mtengo wapatali; ndipo atafika kwa Solomoni anakamba naye zonse za m'mtima mwake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Nafika ku Yerusalemu ndi ulendo wake waukulu, ndi ngamira zakunyamula zonunkhira, ndi golide wambiri, ndi timiyala ta mtengo wapatali; ndipo atafika kwa Solomoni anakamba naye zonse za m'mtima mwake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Idabwera ndi atumiki ambiri ndi ngamira zonyamula zokometsera zakudya, golide wambiri ndi miyala yamtengowapatali. Itafika kwa Solomoni, idamuuza zonse za kumtima kwake.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Inafika mu Yerusalemu ndi gulu lalikulu la ngamira zonyamula zokometsera zakudya, golide wambiri ndi miyala yokongola. Inafika kwa Solomoni ndipo inayankhula naye zonse zimene zinali mu mtima mwake.

Onani mutuwo Koperani




1 Mafumu 10:2
15 Mawu Ofanana  

Ndipo Yehova anapita atatha kunena naye Abrahamu: ndipo Abrahamu anabwera kumalo kwake.


Ndipo mkaziyo ananinkha mfumu matalente a golide zana limodzi mphambu makumi awiri, ndi zonunkhira zaunyinji ndi timiyala ta mtengo wapatali; sunafikenso unyinji wotero wa zonunkhira wolingana ndi uja mfumu yaikazi ya ku Sheba inapereka kwa mfumu Solomoni.


Ndipo Solomoni anamyankha miyambi yake yonse, panalibe kanthu kobisika ndi mfumu kamene sanamfotozere iye.


Ndipo Hezekiya anawamvera, nawaonetsa nyumba yonse ya chuma chake, siliva, ndi golide, ndi zonunkhira, ndi mafuta okometsetsa, ndi nyumba ya zida zake, ndi zonse zopezeka pachuma pake; panalibe kanthu m'nyumba mwake, kapena mu ufumu wake wonse osawaonetsa Hezekiya.


Pamenepo mfumu ya Aramu inati, Tiye, muka, ndidzatumiza kalata kwa mfumu ya Israele. Pamenepo anachoka, atatenga siliva matalente khumi, ndi golide masekeli zikwi zisanu ndi chimodzi, ndi zovala zakusintha khumi.


M'mwemo Naamani anadza ndi akavalo ake ndi magaleta ake, naima pakhomo pa nyumba ya Elisa.


Munthu akayesa kunena nawe mau, kodi udzamva nao chisoni? Koma akhoza ndani kudziletsa kunena?


Chitani chinthenthe, ndipo musachimwe. Nenani mumtima mwanu pakama panu, ndipo mukhale chete.


Mafumu a ku Tarisisi ndi ku Zisumbuzo adzabwera nacho chopereka; mafumu a ku Sheba ndi Seba adzadza nazo mphatso.


mafuta akuunikira, zonunkhira za mafuta odzoza, ndi za chofukiza cha fungo lokoma;


Katundu wa zilombo za kumwera. M'dziko lovuta ndi lopweteka, kumeneko kuchokera mkango waukazi, ndi wamphongo, mphiri, ndi njoka youluka yamoto, iwo anyamula chuma chao pamsana pa abulu, ndi ang'ono zolemera zao pa malinundu a ngamira, kunka kwa anthu amene sadzapindula nao.


Amalonda a ku Sheba ndi a ku Raama anagulana nawe malonda; anagula malonda ako ndi zonunkhira zoposa zilizonse, ndi miyala iliyonse ya mtengo wake, ndi golide.


Ndipo kunali m'kukambirana kwao ndi kufunsana, Yesu mwini anayandikira, natsagana nao.


M'mawa mwake tsono, atafika Agripa ndi Berenise ndi chifumu chachikulu, ndipo atalowa momvera milandu, pamodzi ndi akapitao aakulu, ndi amuna omveka a mzindawo, ndipo pakulamulira Fesito, anadza naye Paulo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa